Innocent Masina Nkhonyo


Chikomekome Cha Mkuyu Ndi Nthano Zina - Poem by Innocent Masina Nkhonyo

CHIKOMEKOME CHA MKUYU

Wolemba: Innocent Masina Nkhonyo

“Monga mphetezi zili zozungulira ndipo zilibe mathero, momwemonso ukwati wanu udzakhale wopanda mathero.” Mwini mawuwatu anali Bambo Rozalio kuchita miyambo yoyera ya ukwati. Kunamveka kululutira kwankokomo kuchokera kwa anthu amene anabwera kudzachitira umboni mwambo woyerawo. Nthungululuzo kunali kuphera mphongo pa zimene ananena munthu wa Mulunguyo. Nawo akwaya sanadikire kukumbutsidwa kuti nthawi yoponya nyimbo m’bwalo inali itakwana. Inayambitsidwadi nyimbo yogwirizana ndi nyengo ya chikondwelerocho. Ngakhale nyimbo yinayambitsidwayo inali imodzi, munali mabvinidwe wosiyanasiyana m’kachisimo. Sizinali zodabwitsa kuona ena akuvina ngati akulumpha jingo janga chifukwa kafungo ka chikokeyani kamkamvekanso cha apo ndi apo pa chipilingu chimkamasula ziunocho. N’zoonadi kuti umu munali m’tchalichi mosafunika fungo la Bibida, komano panalibe mlonda amene akanayima pakhomo la nyumba yopatulikayo kumabweza mbiyang’ambe zimene zinachiona chamzeru kuyamba mwambowo ndi kachakumwa kowawa.. Mmawawutu sikunalinso kovuta kuzindikira njonda zimene zinachita nawo mchezo usiku wapitawo chifukwa zikope za njondazi zimkaonetseratu poyera kuti zinalema n’kusala tulo, zimafuna zitaphimba maso m’dzina lopha tulo.

Aliyense amene anadzachitira umboni ukwati wa Bwideli ndi Jesika anali atavala nkhope ya chisangalalo. Unali ukwati wotukwanitsa mbeta ndi anyamata a m’mphala.. chikondwelero chitafika pa ndime yakuya anachisamutsira ku nyumba kuchoka kutchalichiko. Kunyumbakutu ndiye kunali kukhwasula kwa bwino chemwali mugwedemula sagwada. Anthu akawopsezedwa za kudzimbidwa amayankha amvekere “zathu zomwe izi analipira kale bwana Kita, atsibweni ake a Bwideli”. Nawo akatakwe wodziwa kudukula anali chapoteropo kumasula ziuno motsatana ndi kubangula kwa ng’oma zimenenenso zimkathethetsedwa ndi madolo amanja akucha. Kuwomba m’manja ndi kuvumbulutsa malikhwelu zinali mizati ya tsiku lopambanalo. Ngakhale nsanje inatendera maganizo a anzake ena a Bwideli amene amkanena kuti Jesika anali wa chimasomaso, siyikanaphula kanthu pa ukwatiwo. Inalibe gawo nsanje pa mwambowo poti njonda zansanjezo zinabweranso kudzavinitsa nawo ndukutu m’dzina lotafuna nthumbwana za mbuzi. Ndindani wamphuno zakuthwa akanachita ndwii wosauyatsa ulendo kulondola kumene kunkachokera kafungo kokolonsa mudyo kamene kamkachita adodolido pa mwambo wopambanawo. Panthawiyi n’kuti Bwideli ndi Jesika ali m’nyumba ina kudikira mwambo wosupa. M’nyumbamotu mumkavuvutidwa nyimbo zokankha mwazi wa chikondi zoyimbidwa m’chingerezi. Mutu wa Jesika unali pa chifuwa cha Bwideli kumvetsera nyimbo imene mtima wa wokondeka wakeyo umkayimba. Zonse zosupa zinatha bwino ndipo mwambo wonse unatheranso pamenepa. Ukutu kunali kuyamba kwa ulendo wa Bwideli ndi Jesika m’njira yotchedwa banja.

Masiku woyambilira m’banjali munali chimwemwe cha Adamu ndi Hava m’munda wa Edeni. Patatha zaka zitatu munalowa njoka yotchedwa Mdyelekezi m’munda wamtendele uja. Munali vuto lalikulu m’banjalo limene limavundula chifwilimbiti cha mafunso m’mutu wa Bwideli. Vuto la kusowa kwa mphatso ya mwana ndi limene linalenga mtambo wa chikayiko m’malingaliro a Bwideli. Amkadzidziwa Bwideli kuti analibe vuto lina lirilonse chifukwa anali atayezetsapo ali ku sukulu kuti adziwe ngati analidi mwamuna. Zonse m’thupi mwake zinali bwino. Mvuto linali ndi wokondeka wake Jesika. Komano akanamufunsa bwanji za vutoli poti amkamukonda kwambiri. Anayamba kuwonda Bwideli. Analibe mayankho woyenera pa mafunso amene amkachita yambakatayambakata m’mutu mwake.

Atalema n’kuseza nkhawa kwa zaka zinayi anatulutsa zakukhosi Bwideli. “Daling’i tawona takwanitsa zaka zinayi tili m’banja tsopano koma palibe kamphatso koti ungathe kumakatuma mchere. Kupemphera, tapemphera palibe chikuchitika. Kusala zakudya ndiye wosanena, tawoletsawoletsa nyama m’nyumba muno. Nanga vuto lingakhale chiyani? ” Mmalo mopeleka maganizo ake Jesika anangoyamba kulira. Inalidi nkhani yoliritsa koma kulirako sikunakasintha china chilichonse. Bwideli amkafuna kudziwa chiyambi cha vuto la banjalo. “Daling’i ndikuuza mawa zimene ndikuganiza za vutoli.” Umutu ndi momwe anayankhira Jesika.

Tsiku lotsatira linamutalikira Bwideli. Amangoona ngati akuchedwa kuweruka ku ntchito kwake. Amkafunitsitsa atamva msanga maganizo a Jesika pa za mvuto lawo. Kuthawira ku ntchitoko sizikanathandiza china chilichonse chifukwa pa nthaawiyi naye Jesika anali ku ntchito kwake. Anadikirabe mpakana nthawi yoweluka inakwana. Anauyatsa wakunyumba ndipo sanachedwe kufika chifukwa galimoto imene amkayendetsa pa nthawiyi inamumvera pa nkhani ya liwiro.
Atangolowa m’nyumba anadabwa kuti sanalandilidwe ndi Jesika monga momwe zimkakhalira nthawi zonse. Analunjika kuchipinda poganiza kuti ndikumene akapeze Jesika, kunalibenso wachikondiyo. Atayang’anitsitsa pakama anapezapo pepala. Inali kalata yolembedwa ndi Jesika. Sanachedwe kuyiwerenga kalatayo Bwideli.

Wokondeka Bwideli,
Ndikuthokoza Mulungu chifukwa anandipatsa mwamuna wachikondi ngati iwe. Koma zachinsoni ndinali wachimasomaso ndine. Ndinalephera kukubelekera ana chifukwa ndili kusukulu ndinatayapo mimba. Chifukwa choti njira imene ndinatsata sindimkayidziwa bwinobwino chibelekero changa chinawonongeka kwambiri choncho achipatala anangochichotsa. Sindikufuna kukutayitsa nthawi yambiri n’chifukwa chake ndangoganiza zoti tisiyane basi. Sindikuuza kumene ndikupita chifukwa ngakhale ineyo sindikudziwa. Pomaliza ndikukupempha kuti ukayezetse magazi kuti uyambe kulandira mankhwala wotalikitsa moyo chifukwa ineyo sindilibwino.
Tidzakumana moyo winawo wokondeka wanga wapasi pano ukadzatha.
Ine Jesika.

Ananjenjemera Bwideli ngati wambwandilidwa ndi nyetsi ya magetsi atangowerenga kalatayi. Chiganizo chomaliza cha kalatayo chinamusowetsa mtendere. “Ukayezetse magazi kuti uyambe kulandira mankhwala wotalikitsa moyo” anawelenganso chiganizocho Bwideli. Kenaka anadziyankhulira, “ukadandiuza Jesika.” Misozi inachucha ngati akasupe m’phili la Dzalanyama. Panalibe akanamutonthoza.WAKABWERAKO NDI ZOTENGATENGA

Wolemba: Innocent Masina Nkhonyo*

“Inetu zoti mukafwendekere baba kumeneko sindikufuna, tikudalira inu pa banja pathu pano. Onani ang’ono anuwa akungobwera ndi mandanda kusukulu akumakangosewelakoko” Anakhosomolera munthu wachikulireyo kwinaku akumwazamwaza maso mwaulamuliro pa achichepere amene anamuzungulira panthawiyo, kenaka anapitiliza. “Zikuwonetseratu poyera kuti m’mitu yawoyi alumbwana amenewa mulibe zazikulu koma inuyo chimwene mumawonetsa kuti muli kanthu ndithu m’mutu wobulungirawu, si za mapankezi ayi” Anathulitsa mlango a Timpuzayani chidzulo cha tsiku limenero, kuvinira chinamwali mdzukulu wawo Kambanizithe amene anamusankha ku Yunivesite ya boma. Malipoti amkaveka kuti ku makoleji a Yunivesite makamaka kumene anasankhira Kambanizithe, ku Khansala Koleji, kunali chipwirikiti cha makhalidwe, inali mbuto ya machitidwe achifwilimbwiti chosiyanasiyana. Anali ndi zifukwa zokwaniratu tsibweniwo kupereka mwambo kwa mdzukulu wawoyo kuti asakathyoke mwendo kusukuluko gule akakafika pokoma.

Ananyamukadi m’mawa watsiku linalo Kambanizithe ulendo wa ku Koleji kukayamba kutsinkha nzeru za ukachenjede. Ndindani akanachedwa kukalowa nawo m’gulu la anthu opapira mzeru zakuya? Kwachaka choyamba anali mnyamata ofatsa ndipo anthu womudziwa bwino amkati kufatsako kumkaphatikiziranako ndi kupusa. Atabisala kwa nthawi yayitali ndithu mkachigoba ka khalidweko, zinthu zinasintha atalowa chaka chachiwiri. Zoti anali Kambanizithe Mtupanyama amkadziwa ndi aphunzitsi ake okha akamachonga mapepala ake amayeso. Dzina lake latsopano linali Tiumweretu; mfunda umene umapelekedwa kwa a Mbiyazapolama wokwapula chakumwa chogazula ubongo molapitsa. Chifukwa cha mphulupulu anayambazo, sanasowekelenso kulemba mayeso kuti alowe nawo m’gulu la ‘mafumu’ anthu wovutitsa pa sukulupo, analowadi wopanda wopikisana naye. Moyo wake siumkasiyana ndi wa Lusifala, Ngwazi ya a Demoni. Amati akalikitimula jang’ala wawo amabwera akutukwana. Akafunsidwa za khalidwe lamtudzulo eni akewo amayankha kuti kutukwanako kunali kutsuka m’kamwa. Chovetsa chinsoni n’chakuti amatukwana ngakhale nyumba yosungiramo mabuku pa sukulupo amvekere, “choka khakhakha umatizuza ndi kuwerenga. Dyabulosi, ndiwe wotembeleredwa umatilepheretsa kupapira misozi ya Farao, nthawi tilibe ife! ! ” Nyimbo zambiri za Mulungu anazisintha ndikuyikamo mawu awo otukwana. Analitu woyambitsa kwaya yosokonekerayo anali Kambanizithe

Tsiku lina akanapunthidwa ndi anthu a m’mudzi mwa a chikang’a. Patsikuli Kambanizithe ndi apuludzu anzake anakalowa m’manda am’mudzimo ndikuyamba mtudzu wawo, “Dzuka iwe dziko likukoma ili. Ulesi bwanji? Tadzuka tikamwe mowa.” Ankanena izi akulumphalumpha pa ziliza za m’mandamo. “Kodi udzuka kapena siudzuka? Udzukatu ukusisitira kapena ukulira.” Amkatero kwinaku akuzula mitanda imene inazikidwa pa mitumbira m’mandamo Athokozere amfumu a m’mudzimo amene analeretsa apuludzuwo kwa anthu olusa a m’mudzimo ndithu akanapanda kutelo akanabwelera kusukulu kwawoko zibwano zili m’manja. Zonsezi kwa Kambanizithe ndi anzakewo kunali kunjoya, amkatitu akugoba chisangalaro.

Moyo wa Kambanizithe unali womvetsa chinsoni. Akakwera Basi ya sukulu amaponda pa mpando. Mutu amautulutsa pa zenera akatero amathira maphunzo chilichonse chimene akuchiwona kunja kuyambira mitengo kumalizira nkhuku. Anthu wosawadziwa amatukwanidwanso mosasamala kuti ndi ndani. Anachita zonsezi kwa nthawi ndithu koma tsiku lina anazindikira kuti mowa ndi chitedze ndipo umaliritsa wosasamala.

Linali lachinsanu, monga mwa chizolowezi linali tsiku lobanikira chakumwa. Anakamtungadi Lawidzani pa bara ya Tholo. Koma monga amanena kuti okawona nyanja anakawona ndi Mvuu zomwe, anakayionadi mvuu Kambanizithe kumowako. Kanali kanjole kotchedwa Malita. Chifukwa cha ululu wa Lawidzani sanachedwe kukokerana kuchipinda cha buthulo.

“Kodi watenga chish……..? ” Anafuna kufusa namwaliyo koma sanamalize. “Aaah! Zopusa eti? Ndiwamisala uti amadya nthochi yosasenda? ” Anafunsa ngati wamzeru Kambanizithe kwinaku akuvula buluku. “Palibe.” Anayankha mosaganizira bwino mkaziyo. “Ndiye ngati wamisala amadziwa kuti nthochi timayisenda kaye tisanadye, iwe ndiye ukufuna kundiphuzitsa masamu ake atiwo? Tangoponya bulukuli pachingwepo! ” Analamula mwamphavu Kambanizithe. Zonse zimene mukuganizazo zinatheka usiku wozizilawo……..

Mmawa kutacha sanakhulupilire zimene amkawona Kambanizithe. Anafwikisa m’maso kuchotsa tulo koma palibe chimene chinasintha. Amkawona zenizeni. Buthulo silinali Malita ayi, anali Joyce, mtsikana amene tawuni yonse ya Somba imkamudziwa bwino. Naye Kambanizithe amkamudziwa bwino msungwanayo kuti anali chimbayambaya ndipo zoti anali nako aliyense pa tawunipo amkadziwa. Analira ngati wafedwa mwana wamwamuna. Anatukwana mowa umene unamupusitsa. Nchifukwa chiyani mowa unamupangitsa Kambanizithe kuona Joyce ngati kamngelo kothotholedwa m’dimba la maluwa a chiyembekezo.

Mosakhalitsa analisiya buthu lija m’chipindamo likumwetulira. Panalibe chifukwa chopelekera ndalama ndi ndani akanakhala mchipindamo kumagula imfa? Ankadziwa bwino kuti wayitenga ndipo anali ndi zifukwa zokwanira zokhetsera misozi. Atafotokozera anzake za nkhawa yakeyo, sanamubisire Chichewa. Anamuuza mwachimvekere kuti anakolonsawo anali mabvu nkhomola. Ena anayamba kulapa pomwepo kuti sadzamwanso mowa moyiwala ndi dzina lawo lomwe chifukwa zimene zinamuchitikira Kambanizithe zingathenso kudzawachitikira tsiku lina ngati sasintha mkhalidwe woipawo. Koma haa mabvuto anali ndi Kambanizithe. Analitu atavulala kale ndipo kwa iye amkangodikira tsiku limene mphulupulu zakezo zidzayambe kumubweletsera zitete zodzala ndi zipatso

Chifukwa cha maganizo azimene zinamuchitikilazo komanso zimene amkayembekezera kuti zimuchitikira, sizimamuyenderanso bwino m’kalasi Kambanizithe. Chaka chachitatu chitatha, anamuchotsa sukulu atalakwa mayenso achibweleza amene amapelekedwa kwa ophunzira wolakwa mayeso woyamba. Anapitadi kwawo koma atangokhala masabata awiri, chifuwa chinayamba. Kenaka kutsekula m’mimba, kenaka mbiri inayamba kuwanda pamudzipo kuti wakabwerako ku Koleji ndi zotengatenga. Aliyense amkadziwa bwino chimene chinamutsalira Kambanizithe. Zinali zoliritsa.


*Innocent Masina Nkhonyo
Chancellor College
P.O. BOX 280
Zomba
09268999
< br>
NKHUYU ZODYA MWANA

WOLEMBA: INNOCENT MASINA NKHONYO

“Tabweretsani zingwe tikwidzinge mayi wa nthyambayi.” Linaponyedwa lamulo ngati mphezi kuchokera kwa mkulu amene amatsogolera njonda zolusanzo. Zikuonetsa kuti lamuloro linagwadi pa mapilikaniro akumva chifukwa sipanatenge nthawi yayitali kuti zingwe zotchedwa zikondo zifike pamalopo. “Tabweretsa manja kumbuyo mayi wa mfiti! Usandiphulitsetu ngozi ine! ” Analamulanso mkulu uja milomo ikundenguka ndi ukali. Amkapereka malamulowo kwinaku akupulumutsa makofi amene amkatera pa masaya a makwinya amayi uja ngati makwangwala m’munda wa mtedza. Nawo amene anali ndi mitima yokhakhalala ngati m’manja mwa nyani uja wotchedwa chiyendayekha amkathandiza mkulu uja kupamantha mayiyo mopanda chinsoni. Panthawiyi n’kuti a Namsani atakhumata mokodola mitunga ya chinsoni. sakathanso kuphelera kapena kuzinda mapama amkapulumutsidwa pamalopo. Akanazinda bwanji ndi chipiringu chimene chinasankha kudzaongola nawo manja pa mayiyo. Ngakhale ena samadziwa chifukwa chenicheni chimene chimawayenereza kumenya a Nansani, samalabadira kufusa chimene chinachitika koma amangofikira kuponya zibakera mwa mayiyo ngati a katswiri a nkhonya.

Magazi amkachucha mkamwa ndi mphuno mwa mayiyo ngati liwende la tonde watsoka amene wasankhidwa kuponyedwa pa khala kuti anthu wodzachitira umboni mwambo wa ukwati achotsere khambi mkamwa. “Imilira! Utilondolere kumene kuli chigandanga chakocho.” Analamulidwa kuyimilira a Namsani, koma analibe mphamvu zodzukira. Akanayima bwanji poti manja anali kumbuyo atawakwidzinga nyakula. Kulephera kuyima kunapangitsa kuti alandire zikwapu zimene ng’ombe yokanika kuyenda pangolo imalandira. Panali kumenya mwachisawawa, aliyense ufuna kuwongola manja anali wolandiridwa. “Mayo mundipheranji? ! ! ” Analira ngati mwana gogoyo. Mmawu agogoyo munali ululu umene aliyense wobadwa kwa munthu anayenera kuumva. “Takasiyani kankhalambaka kadzuke kaye” Kumenyakodi kunasiyika kaye potsatira lamulori kuchokera kwa mkulu amkatsogolera uja. Ndikhulupilira kuti pakanapanda lamuloro palibe akanasiya kuwumbudza gogoyo. Ndinaona misozi ikuchucha mmaso mwa a Namsani. Ululu umene amkamva panthawiyi unali chifukwa chokwanira chokhetsera misozi. Chinsoni changa pa mayiyo chinafika pa ndime yakuya ndi mmene amkaonekera. Ngakhale ndinali ndisanadziwebe chimene mayiyo analakwa kuti alangidwe moteromo, ndimkakhulupilirabe kuti panalibe chilungamo pa chilangocho.

Chikhumbokhumbo chofuna kudziwa tchimo limene mayiyo anachimwa kuti alandire zowawazo chinandigwera, koma ndindani akanandiuza zoona poti ambiri mwa anthu amene anali pamalopo amawonetseratu kuti amagwirizana nacho chilangocho. Ndikanapanda kuona wina amene amaonetsa kuti samatenga nawo mbali iliyonse, ndikanachoka pa malopo wosadziwa chimene chinakodola mavuto a mayiyo. Ndinayitanadi mkulu wina amene samaonetsa chidwi kutenga nawo gawo pa zochitikazo ndipo anandifotokozera chilichonse mosalumpha chinyanja. Mkufotokoza kwakeko anandiuza kuti ngakhale mayiyo amalandira chilangocho anali wosalakwa. Atanena mawuwa ndinayipitsa nkhope yanga. Wofotokozayo anadziwa kuti zimene ananenazo zinali ngati zopanda mzeru kwa ine. Ndindani akanakhulupilira zimenenezo? Ndindani akanalora kumenyedwa popanda chifukwa? Ilitu ndi funso limene anakhala ngati waliona m’maganizo anga chifukwa analiyankha ndisanalifunse. Anandifotokozera kuti anatsotsola mavuwo anali mwana wa mayi amkapunthidwayo. Sindinadabwe ndi chibvumbulutsocho, kangapo konse ndinamvapo anthu amkamenya mayi uja akumulamula kuti awalondolere kumene kunali mwana wake. Ndinakhala tcheru pamene mkulu uja amafotokoza koma kamutu kangaka ndimkagwedeza cha apo ndi apo, kumukopa wofotokozayo kuti akambe zambiri. Ndindani amene safuna kumva zambiri pa chipwirikiti ngati chimenechi.

Anapitiriza kuti mwana wa mayiyo anafuna kukaba m’dimba la mkulu wina. Mwatsoka kaya mwayi kapsalayo anapezeleredwa m’dimbamo ndi mwini mbewuzo. Ndiyetu kunali kulimbana ndi kudilizirana pansi pakati pa mwini dimbalo ndi tsizinamtoleyo. Zotsatira za kulikhirana pansiko ndi zimene zinayitanira mayiyo mabvutowo. Ngati mwana wophunzira kumene zinthu ndinapempha wofotokozayo kuti alongosole bwino kumapeto kwa nkhani yakeyo. Sanandibisire zoti mwana wa mayiyo, mbava ija, inapha mwini dimbalo ndikuthawa. Ndinauzidwanso kuti mbavayo yinazindikiridwa ikuthawa ndi anthu ena wongodziyendera. sipamafunikanso wofotokozayo kundiuza kuti anthu anabwera kudzalanga mayi wa tsizinamtoleyo anali abale ake a munthu wophedwa uja kuyipidwa ndi imfa ya mbale wawo. Ndinachipeza chifukwa cha mkwiyo wawo. Chinali chokwanira.

Koma…….koma n’chifukwa chiyani anaganiza zolanga mayiyo mmalo mokasaka waupanduyo kumuphunzitsa khalidwe koma wosavuta mayiyo? Ilitu linali funso limene linandipangitsa kukumbukira mwambi woti nkhuyu zodya mwana zimapota akulu. Ndinawamvera chinsoni a Namsani. Amalandira zowawa chifukwa cha mphulupulu za mwana wawo. Amafera unakubala a Nansani. Misozi inalengeza m’maso mwanga nditakumbukira mphulupulu zanga zimene zinawabweretseranso mabvuto mayi anga okondeka a Naluwa. Ndinamuthokoza wofotokozayo chifukwa chondiwunikira pa zimene zinachitikazo. Sindimkafuna kuti ayimebe pamene ndinali inepo chifukwa akanatero akanaona mosavuta misozi imene panthawiyi inali itatsala pang’ono kusiyana ndi maso anga ndikutsetsereka pa masaya anga. Sindinakhalitse pamalopo chifukwa ndikawaona a Namsani ndimakumbukira mayi anga. Ndimkapita kunyumba kwanga nkhope nditagwetsa ngati nyau yotuluka m’bwalo isanafupidwe kangachepe. Ndinali ndi zifukwa zokwanira zogwetsera nkhope. Ndimkadziwa kuti mayi anga wokondeka a Naluwa anatsamaya ndisanawapepese pa mphulupulu zanga zimene zinawasautsa ali moyo.

Mwinamwake, kwinakwake, nthawi ina yake ndidzapempha chikhululukiro chawo tikadzakumananso. Mzimu wawo uwunse mu mtendere, ilitu linali pemphero limene linakandifitsa pa nyumba panga.

NKHUYU ZODYA MWANA

WOLEMBA: INNOCENT MASINA NKHONYO

“Tabweretsani zingwe tikwidzinge mayi wa nthyambayi.” Linaponyedwa lamulo ngati mphezi kuchokera kwa mkulu amene amatsogolera njonda zolusanzo. Zikuonetsa kuti lamuloro linagwadi pa mapilikaniro akumva chifukwa sipanatenge nthawi yayitali kuti zingwe zotchedwa zikondo zifike pamalopo. “Tabweretsa manja kumbuyo mayi wa mfiti! Usandiphulitsetu ngozi ine! ” Analamulanso mkulu uja milomo ikundenguka ndi ukali. Amkapereka malamulowo kwinaku akupulumutsa makofi amene amkatera pa masaya a makwinya amayi uja ngati makwangwala m’munda wa mtedza. Nawo amene anali ndi mitima yokhakhalala ngati m’manja mwa nyani uja wotchedwa chiyendayekha amkathandiza mkulu uja kupamantha mayiyo mopanda chinsoni. Panthawiyi n’kuti a Namsani atakhumata mokodola mitunga ya chinsoni. sakathanso kuphelera kapena kuzinda mapama amkapulumutsidwa pamalopo. Akanazinda bwanji ndi chipiringu chimene chinasankha kudzaongola nawo manja pa mayiyo. Ngakhale ena samadziwa chifukwa chenicheni chimene chimawayenereza kumenya a Nansani, samalabadira kufusa chimene chinachitika koma amangofikira kuponya zibakera mwa mayiyo ngati a katswiri a nkhonya.

Magazi amkachucha mkamwa ndi mphuno mwa mayiyo ngati liwende la tonde watsoka amene wasankhidwa kuponyedwa pa khala kuti anthu wodzachitira umboni mwambo wa ukwati achotsere khambi mkamwa. “Imilira! Utilondolere kumene kuli chigandanga chakocho.” Analamulidwa kuyimilira a Namsani, koma analibe mphamvu zodzukira. Akanayima bwanji poti manja anali kumbuyo atawakwidzinga nyakula. Kulephera kuyima kunapangitsa kuti alandire zikwapu zimene ng’ombe yokanika kuyenda pangolo imalandira. Panali kumenya mwachisawawa, aliyense ufuna kuwongola manja anali wolandiridwa. “Mayo mundipheranji? ! ! ” Analira ngati mwana gogoyo. Mmawu agogoyo munali ululu umene aliyense wobadwa kwa munthu anayenera kuumva. “Takasiyani kankhalambaka kadzuke kaye” Kumenyakodi kunasiyika kaye potsatira lamulori kuchokera kwa mkulu amkatsogolera uja. Ndikhulupilira kuti pakanapanda lamuloro palibe akanasiya kuwumbudza gogoyo. Ndinaona misozi ikuchucha mmaso mwa a Namsani. Ululu umene amkamva panthawiyi unali chifukwa chokwanira chokhetsera misozi. Chinsoni changa pa mayiyo chinafika pa ndime yakuya ndi mmene amkaonekera. Ngakhale ndinali ndisanadziwebe chimene mayiyo analakwa kuti alangidwe moteromo, ndimkakhulupilirabe kuti panalibe chilungamo pa chilangocho.

Chikhumbokhumbo chofuna kudziwa tchimo limene mayiyo anachimwa kuti alandire zowawazo chinandigwera, koma ndindani akanandiuza zoona poti ambiri mwa anthu amene anali pamalopo amawonetseratu kuti amagwirizana nacho chilangocho. Ndikanapanda kuona wina amene amaonetsa kuti samatenga nawo mbali iliyonse, ndikanachoka pa malopo wosadziwa chimene chinakodola mavuto a mayiyo. Ndinayitanadi mkulu wina amene samaonetsa chidwi kutenga nawo gawo pa zochitikazo ndipo anandifotokozera chilichonse mosalumpha chinyanja. Mkufotokoza kwakeko anandiuza kuti ngakhale mayiyo amalandira chilangocho anali wosalakwa. Atanena mawuwa ndinayipitsa nkhope yanga. Wofotokozayo anadziwa kuti zimene ananenazo zinali ngati zopanda mzeru kwa ine. Ndindani akanakhulupilira zimenenezo? Ndindani akanalora kumenyedwa popanda chifukwa? Ilitu ndi funso limene anakhala ngati waliona m’maganizo anga chifukwa analiyankha ndisanalifunse. Anandifotokozera kuti anatsotsola mavuwo anali mwana wa mayi amkapunthidwayo. Sindinadabwe ndi chibvumbulutsocho, kangapo konse ndinamvapo anthu amkamenya mayi uja akumulamula kuti awalondolere kumene kunali mwana wake. Ndinakhala tcheru pamene mkulu uja amafotokoza koma kamutu kangaka ndimkagwedeza cha apo ndi apo, kumukopa wofotokozayo kuti akambe zambiri. Ndindani amene safuna kumva zambiri pa chipwirikiti ngati chimenechi.

Anapitiriza kuti mwana wa mayiyo anafuna kukaba m’dimba la mkulu wina. Mwatsoka kaya mwayi kapsalayo anapezeleredwa m’dimbamo ndi mwini mbewuzo. Ndiyetu kunali kulimbana ndi kudilizirana pansi pakati pa mwini dimbalo ndi tsizinamtoleyo. Zotsatira za kulikhirana pansiko ndi zimene zinayitanira mayiyo mabvutowo. Ngati mwana wophunzira kumene zinthu ndinapempha wofotokozayo kuti alongosole bwino kumapeto kwa nkhani yakeyo. Sanandibisire zoti mwana wa mayiyo, mbava ija, inapha mwini dimbalo ndikuthawa. Ndinauzidwanso kuti mbavayo yinazindikiridwa ikuthawa ndi anthu ena wongodziyendera. sipamafunikanso wofotokozayo kundiuza kuti anthu anabwera kudzalanga mayi wa tsizinamtoleyo anali abale ake a munthu wophedwa uja kuyipidwa ndi imfa ya mbale wawo. Ndinachipeza chifukwa cha mkwiyo wawo. Chinali chokwanira.

Koma…….koma n’chifukwa chiyani anaganiza zolanga mayiyo mmalo mokasaka waupanduyo kumuphunzitsa khalidwe koma wosavuta mayiyo? Ilitu linali funso limene linandipangitsa kukumbukira mwambi woti nkhuyu zodya mwana zimapota akulu. Ndinawamvera chinsoni a Namsani. Amalandira zowawa chifukwa cha mphulupulu za mwana wawo. Amafera unakubala a Nansani. Misozi inalengeza m’maso mwanga nditakumbukira mphulupulu zanga zimene zinawabweretseranso mabvuto mayi anga okondeka a Naluwa. Ndinamuthokoza wofotokozayo chifukwa chondiwunikira pa zimene zinachitikazo. Sindimkafuna kuti ayimebe pamene ndinali inepo chifukwa akanatero akanaona mosavuta misozi imene panthawiyi inali itatsala pang’ono kusiyana ndi maso anga ndikutsetsereka pa masaya anga. Sindinakhalitse pamalopo chifukwa ndikawaona a Namsani ndimakumbukira mayi anga. Ndimkapita kunyumba kwanga nkhope nditagwetsa ngati nyau yotuluka m’bwalo isanafupidwe kangachepe. Ndinali ndi zifukwa zokwanira zogwetsera nkhope. Ndimkadziwa kuti mayi anga wokondeka a Naluwa anatsamaya ndisanawapepese pa mphulupulu zanga zimene zinawasautsa ali moyo.

Mwinamwake, kwinakwake, nthawi ina yake ndidzapempha chikhululukiro chawo tikadzakumananso. Mzimu wawo uwunse mu mtendere, ilitu linali pemphero limene linakandifitsa pa nyumba panga.*Innocent Masina Nkhonyo
Chancellor College
P.O. Box 280
Zomba

09268999< br>
CHALA SICHILOZA MWINI

Wolemba: Innocent Masina Nkhonyo

“Akulira mwana, heee!
Akulira mwanaaa kudambweee!
Gwira nkhuku ukaneneee!
Akulira mwana heee!
Akulira mwanaaa kudambweeee!
Gwira nkhuku ukaneneeee! ”

Kunali kuyimba kosokoneza bata ndi mtendere zimene zinafungatira usikuwo. Ndi mmene amkavekera mawuwo aliyense m’mudzimo anamuzindikira mwini mawuwo. Ngakhale nyimboyo imkayimbidwa mosaphophonyetsa mawu, sikunali kovuta kudziwa kuti katswiri amkalikitimula nyimboyo anali atakonkhako matoti angapo a misozi ya Farao. Zikuonetsa kuti namatetule woyimbayo amkati akagwa chifukwa cha ukali wa delundeyo, amadukiza kaye nyimbo yakeyo kenako amapitiriza kuyimba pamene analekezera akadzukilira. Kuwuwa kwa agalu sikunapereke mantha aliwonse kwa njonda inachiona cha mzeru kusokoneza usikuwo. Kuwuwa kwa agalu kunali kulandira njondayo m’mudzimo ngati Karonga. Inasinthira kaye nyimbo njondayo isanayambe kugeya mwano monga inkachitira masiku wonse ikatibula zakumwa zowawazo.
“Ukungokhala uli cheteee
mwendo wapachika umati n’chite kukuuzaaa!
Susiyapo mbewu pano!
Ukungokhala ulicheteee
mwendo wapachika umati n’chite kukuuzaa!
Susiyapo mbewu pano! ”

Atakhutitsidwa kuti wayimba mokwanira kwa usiku umodzi Katambalale, poti ndiye linali dzina la njondayo, anayamba kulalika zimene chipembedzo cha jang’ala chimaphunzitsa. Kudzandira polalika chinali chizindikiro chokwanira choti wolalikirayo anali wobatizidwa mu mpingo wakachasu. “Agalu, atchisi mungandiuze chiyani chamzeru? ! ” Anayamba ndikufusa funso la mwano mu ulalikiwo. “Uwuwuuwu! Chiyani? Ukuwuwa ambuyako? ! ” Amanena izi akutola mwala kuti aphunzitse mkhalidwe galu wina amene amauwabe panthawiyi. Ataponya mwalawo anagwa thii Katambalale ngati mtengo wa matondo. Analitu atathima mopyola muyeso, analibe mphamvu ngakhale zolasira galu. Anadzuka koma movutika kwambiri kwinaku akutulutsa zichewa zimene zimaloleradwa kutchulidwa mwaufulu ku chinamwali kokha. Kenaka anapitiliza kugawa mawuko. “Ndikufuna mudziwe inu anthu opepera.” Anakweza mawu ake kuti aliyense amve zauthenga umene amkafuna kugawana nawo usikuwo. “Ine m’mudzi mwanu muno mwachulukamo anthu a Edzi muona ndikuchokerani! ” Uthengawu unafika m’mitima ya anthu amene amkamvetsera kacheteche za mtudzuzo mnyumba zawo. Unali wuthenga wodzetsa mkwiyo m’mitima ya anthuwo. Koma akanamutani Katambalale poti anali msuweni wa amfumu a m’mudzimo. Paja amati akakhala pa mkhate sapheka anthu am’mudzimo sakanasintha zeru za mwambiwu. Anamusiya katambalale kuti azigeya mwano wakewo. “Ati tang’atang’a ngati zili bwino, mwatsala enanunso tikakuyikani. Mukamanenepa nako mukumawona ngati ife sitimakudziwani? Hehedee! Ati kubisala pachipande.” Anaseka Katambalale ngakhale zimene amanenenanzo sizinali zoseketsa. “Yagwa muufa, yagwa muufa chiyani? Enafe nanga tikuyipewa bwanji? Asa fotseku mwapanga bwanji anthu wopenga? ! ” Anapitiliza kusokola anthu wokhudzidwa ndi mliriwu m’mudzimo. “Mawa ndikakutengelani chikalata ku chipatala ndidzidzakuonetsani ngati umboni kuti enafe timadzisunga paja zitsiru za kwa Nkhukuyasokera mumakhulupilira pokhapokha mukaona.” Umutu ndi mmene anamalizira ulaliki wa usiku umenewo Katambalale. Kukanakhalanso buku lopatulika ku chipembedzo cha zidakwa bwezi tikuti Katambalale watsekano buku loyeralo. Anapita kukagona wosadya chakudya chimene anamusungira usikuwo. Akanachedweranji kumatsinkha khwanya ndi mkamwa mwake mwa mowa mofuna zankhuli? Kanyenya amene anadya kuchakumwacho anali atamukwana.

Mmawa kutacha anasungadi lonjezo lake lija Katambalale. Analawilira kukayezetsa magazi ndi cholinga choti azidzawalira anthu m’mudzimo kuti anali munthu wa ngwiro. Anali woyambilira kuyezedwa patsikulo. “Kodi a Katambalale alipo apa? ” Anafunsa namwino wina kwinaku akudzikakamiza kuwonetse nkhope ya sangala. Anakweza dzanja Katambalale kutsimikiza kuti mwini dzinalo anali iyeyo. Analamulidwa kulondola namwinoyo. Atalowa anamulozera pokhala. Nthumazi inamugunda kwa nthawi yoyamba, Inali nthawi ya chiwerunzo. Anadzilimbitsa mtima poganiza mmene anali atakhalira kunkhani ya za m’banjayi. Anali munthu wokhulupilika koma amayenerabe kuchita mantha, sichinalitu chiwerewere chokha chimene akanatengera nthenda yowopsa ija.

“Ndikhulupilira kuti mwakozeka kumva zotsatira zanu bambo.” Anatsekulira namwino uja mwachikoka kwambiri. “Koma ndisanakuuzani zotsatirazo ndili ndi chikhulupiliro kuti mukukumbukira zimene ndinakuuza zija ndisanayeze magazi anu.” Anagwedeza mutu Katambalale kumutsimikizira namwinoyo kuti amakumbukira zonsezo. Nthawi ya tiuzane tchutchutchu inakwana ndipo anatsekula pakamwa namwino. Anamva ngati timadzi tikuyendelera kuchokera mkhwapamu kutsikira cha mmbali mwa mimbayi. Analitu madzi wotchedwa thukuta kuchitira umboni za kuwopsa kwa nyengoyo. “Tati titayeza magazi anu mosamala ndithu tapeza kuti inuyo kachilomboko muli nako.” Anavumbulutsa zotsatira namwinoyo maso ali gaa pa mtunda. Anadumpha pampando ndi mantha wosakanikirana ndi ukali Katambalale. “Sizingathekeee! ! ! ” anabangula ngati mkango mwana wa mwamuna. “Ndati sizingatheke ngakhale pang’ono! ” Analamula kuti ayezedwenso. Zotsatira sizinasinthe, anali nako basi.

Anatuluka m’kachipindamo manja ali ku nkhongo. Zoti pamakhala malangizo munthu akauzidwa zotsatira za magazi ake, kwa Katambalale sizikatheka. Akutuluka m’chipindamo anaona azimayi ena akuona nyuzipepala. Anali atamvala nkhope zokwiya wonsewo. Atawonetsetsa pa pepalapo anadziwonera mutu wa nkhani ina Katambalale. “Asumilidwa chifukwa chosagwiritsa ntchito lezala mosamala.” Unatero mutuwo. Atawonetsetsa nkhani yonseyo anamvetsa chimene chimachitika. Azimayi ena anasumira sing’anga wina chifukwa choti anawapatsira kachilombo koyambitsa matenda a Edzi atawatema mphini ndi lezera woti watemera anthu ambiri. Chimene chinamugowola nkhongono Katambalale ndi tsiku limene lezalayo anagwiritsidwa ntchito, linalinso tsiku limene Katambalaleyo anakatemedwa mphini ndi sing’anga yemwe uja anatema azimayiyu. Kukayika konse zoti ali nako kunachoka. Zinali zachidziwikire kuti anatenga kachilomboko tsiku limenelo. Nkhawa inamugwira. Akanena chiyani kumudzi kwawo poti analengeza usiku zija atapapira delunde anthu amayembekezera zotsatira zake. Amkapita kumudzi kwawo akulingalira kuti ndi bwino nthawi ino yovuta kumasiya chiwerunzo chonse m’manja mwa Mulungu poti kumene kwatsala tchire ndikumene moto umawolokera.


*Innocent Masina Nkhonyo
Chancellor College
P.O Box 280
Zomba

09268999
< br>
AKANATANI BAMBO MAYIKOLO

WOLEMBA: INNOCENT MASINA NKHONYO*

Kamphepo kovinitsa nthambi za mitengo gule wa vimbuza kamkawomba wosati mwa ukali koma mowonjezera kukometsa tsikulo. Nako kadzuwa kachotsa chithuzithuzi chako ukunding’ambira gombeza kamkathwanima mopatsa funso la ndidzazime ndidzatsikire ku nkhadze ine? Mbalame kukhala chikhalidwe chawo chokometsa chilengedwe zimkachita phuphuluphuphulu kutakasa mapiko, miluzi ili pakamwa kufikitsa kukoma kwa tsikulo pa ndime yakuya. Sizinalitu zodabwitsa kuwaona abambo Mayikolo atavala nkhope yachimwemwe patsikulo. Nawo monga munthu wachilungamo, wansembe wosankhidwa wake wa Mulungu, anali wokhutira ndi luso la Chauta, mwini kuthambo, amene anakhuthulira chinsomo chodyetsera maso patsiku lowerukalo. Mwinjiro umene anaponya pathupi pawo mmawa wokomawo umkachitira umboni za kupatulika kwa malo amene munthu wa Mulunguyo amayendapo, panali pa khonde pa tchalitchi cha Mtimawopatulika.

Tsikuli limakwanitsa miyezi iwiri chimwalilireni amayi a bambo Mayikolo, a Nasuluma, amenenso amkakhala pafupi ndi pa tchalichi chimene bambo Mayikolo amatumikira. Mzimu wa mayiyo uwuse mu mtendere, anafa ifa yozuzika kwambiri a Nasuluma. Kunali kovuta kwa bambo Mayikolo kuyiwala za nkhalwe zimene anaziona a Nasuluma pa imfa yawo. Anachitatu chowapha mayiwo ngati katumbu wogwidwa akusakaza nsomba m’dziwe la mlimi wa nsomba. Chomvetsa chinsoni n’chakuti awupanduwo anadula mawere a mayiyo. Sizikudziwika kuti anadula ziwalozo mayiyo ali moyo kapena ataphedwa kale. Zonsezitu zimadzetsa mkwiyo wosakanikirana ndi chinsoni kwa Bambo Mayikolo. Ngakhale panachitika kalondolondo wofuna kumbwandira a khakhakha anachita zaupanduzo, palibe ndi mmodzi yemwe amene amkadziwa a misiri anayikapo dzanja pa imfa ya mayiyo. Pa miyezi iwiri yonseyi sizimawayendera bambo Mayikolo. Ngakhale anali wansembe amene anthu amamasuka naye podzamutulira nkhawa zawo, anapemphedwa kuti apume kaye kugwira ntchito zina. Panalibe kuchitira mwina koma kupumula kaye ntchito zina. N’zachidziwikire kuti imfa ya a Mayi awo inawasautsa kwambiri.

Pamene bambo Mayikolo amaganizirabe za chikondi cha Mulungu pa tsikulo, pa tchalichipo panafika munthu wina. Amkalunjika kumene kunayima bambo Mayikolo. Mmene amkaonekera mkuluyo sizimafunika mpakana katswiri wophunzira za maganizo a anthu kuzindikira kuti mkuluyo anali ndi nkhawa yowopsa. Amkapita kwa munthu woyenera. Ndindani m’deralo amene samkadziwa kuti munthu yekhayo amene anali ndi mphatso yomasula anthu ku singa zosiyanasiyana anali bambo Mayikolo?

Anamulandira bwino munthuyo. Ngakhale sanamuuze kuti akhale womasuka koma nkhope yasangala ya bambo Mayikolo inamutsimikizira kuti anali wolandiridwa. “Tigawanetu zimene mwatibweletsera paja amati mlendo ndiye ayenda ndi ka mlomo kakuthwa” anatsekulira ndi nthabwala bambo Mayikolo kufuna kudziwa chimene chinakokera mkuluyo kwa iwo m’mawawo. “zoonadi bambo ndili ndi nkhawa yayikulu. Ndine munthu woyipitsitsa sindikudziwa ngatinso ndingapulumuke” mawuwa amkatuluka pakamwa pa mlendo uja koma nkhope yake yokutidwa ndi chikayiko imkakamba zambiri kuposa zimene zimkatuluka pakamwapo. “Khala womasuka mwana wanga, palibe mphulupulu imene Yahweh sangakukhulukire. Pa……… amati ngakhale tchimo lanu litakhala lofiyira ngati magazi lidzayera ngati matalala pamangofunika kudzichepetsa basi” anagwiritsa ntchito lembo m’buku loyera bambo Mayikolo kuyitsimikizira nkhosa yotayikayo kuti ambuye ndiwachifundo amatikhululukira tchimo lina lirilonse. Wofuna chikhululukiroyo anagwirizana ndi fundo yoti adzichepetse kuti machimo ake wofiira ngati magazi ayeretsedwe ngati ngati matalala. Njira yokhayo yodzichepetsera pamaso pa Yehovah inali kulapa machimo ndipo bambo Mayikolo pokhala wansembe amene amkathandiza anthu ambiri pa nthawi yolapa inawakondweretsa kwambiri nkhaniyo. Monga kholo lirilonse lofunira zabwino mwana wake limasangalala mwana wake akazindikira kulakwa kwake ndi kulapa, bambo Mayikolo anali ndi zifukwa zokwanira zomwetulira patsikulo chifukwa anali kholo mu uzimu ndipo patsikuli nkhosa yotayika inali itapezeka.

Monga mwa chizolowezi pa ntchito yawo ya unsembe anakalowa ndi munthu uja mkachipinda mmene amalapitsiramo machimo. Kulapako kunayambika potsata malamulo a mpingo. Zimene zimanenedwa mkachipindamu zimathera momwemo. Wolapayo amalapa kwa Mulungu ndipo wansembe amangokhala ngati mthandizi chabe. Bambo Mayikolo amkazidziwa zonsezi. Anali atasunga malamulowa kwa zaka khumi kuchokera tsiku limene analandira udindo waukuluwo, unsembe. Ichitu chingathe kukhala chitukwa chimene chimakoka anthu ambiri kupita kwa bambo Mayikolo. Munalitu bata lodzetsa mantha mkachipindamo. “Sindikudziwa kuti chimkandichitikira ndi chiyani, ndinalakwira Mulungu komanso anthu osayenera kuwalakwira” amkadandaula motero wodzalapa uja koma bambo Mayikolo anamulimbikitsa. Anampatsa zitsanzo zambiri za anthu amene anali wochimwa kwambiri poyamba koma anatembenuka. Saulo wa ku Damasko anali chimodzi mwa zitsanzo zimene zinaperekedwa. Panalibe chifukwa chowopera kulapa. Ngati Mulungu anakhulukilira Saulo, nkhawena yofuna kupulula a khristu, ndiye akanalephera bwanji kukhululukira nkhosa inagwada pamanso pa bambo Mayikoloyi? Inalimba mtima nkhosayo ndikuyamba kuulula machimowo m’dzina lolapa.

“Bambo wanga thandizeni kulapa machimo anga moyenera, machimo anga nawa: ndakhala ndikuba komanso kupha anthu mwachisawawa.” Ananena machimo ambiri wodzalapayo, zikuwonetsa kuti anadzazidwa ndi mzimu woyera chifukwa amkanena izi akuchucha misozi. Panalibe chifukwa chosatulira nkhawa zonse m’manja mwa Mulungu. Panthawiyi bambo Mayikolo amkangomvetsera koma chinachake chinawasokoneza mkumvetsera kwawoko. “Andikhululukire Mulungu wa Daniele chifukwa amayi anu aja ndinapha ndi ine bambo.” Sanakhulupilire zimene mapilikaniro awo amatumiza ku ubongo bambo Mayikolo. “Chani? ! ! ! ” Anafunsa akuyimilira pa mpando pamene anakhala. Misozi inachucha m’maso mwa bambo Mayikolo. Chigawenga chimene chinapha mayi wawo ndi kuwadula mawele chinali chigwadire patsogolo pawo. Mkwiyo umene umkawoneka mmaso mwa bambo Mayikolo unathandiza wodzalapayo kuzindikira koma mochedwa kwambiri kuti anadzatula nkhawa zakezi kwa munthu wolakwika. Bambo Mayikolo monga munthu wina aliynse analinso ndi zinthu zina zimene zimawapsetsa mtima ndipo imfa ya mayi wawo inali chimodzi mwa zinthuzo. “Wati chiyani? ! ! ” Anamaliza funsolo manja awo ataponya kale pakhosi pa wodzalapayo. Anamukanyanga ndipo amapotokola khosilo misozi ikutsika mwaukali mmasaya mwawo bambo Mayikolo. Analitu atalumira mano. Ngakhale wodzalapayo anayesa kuphiliphitha sizinathandize. Manja amene anamugwirawo sanali amuntha walebedelebede, bambo Mayikolo anali ndi dzitho. Ndi ukali umene anali nawo pa nthawiyo kuphatikiza dzithodzo, ndi amuna asanu anyonga zawo amene akanakwanitsa kupulumutsa khosi la mkuluyo m’manja mwa bambo Mayikolo. Koma haa zachinsoni panalibe amuna asanu anyongawo………………

Panthawi imene anthu amabwera kudzawona chimene chimachitika n’kuti moyo wina utasiyana kale ndi dziko lapasi. Nkhani itafotokozedwa anthu anamvetsa chimene chinapangitsa munthu wa Mulunguyo kuchita zinthu ngati chinkhanira. Zinali zachidziwikire kuti analephera ntchito yawo bambo Mayikolo posasunga chinsinsi chifukwa chowawidwa mtima. Komano akanatani bambo Mayikolo poti nawo ndi munthu womva zowawa nthawi zina ndi zokomanso nthawi zina.

*Innocent Masina Nkhonyo
Chancellor College
P.O. BOX 280
Zomba

09268999
< br>MAPANGA AWIRI AMVUMBWITSA

WOLEMBA: INNOCENT MASINA NKHONYO*

Anatuluka mu ofesi Mofolo nkhope atagwetsa ngati namwali wongotuluka kumene m’tsimba atatha kuvuvutidwa ndi mlango wa anamkungwi. Aliyense amene anali pa makonde a ofesiyo anadziwiratu kuti mzawoyo anakumana ndi mavunkhomola amene anamutsopa chibwana chonse mopanda chinsoni. Ndindani akanakayikira kuti mpini watsoka unali utazuzunda chipumi cha Mofolo ndi mmene amkasisimiramo? “Sindifuna kugwetsa kampani ndi anthu wosadalirika! .” Uyu anali bwana wa pamalopo kutuluka mu Ofesi munatuluka Mofolo muja. Mapepala amene anali m’manja mwa njonda ya ulamuliroyo amkasonyezeratu poyera kuti bwanayo anali ndi ntchito yayikulu yosayinira mapepalawo osati kumalimbana ndi apuludzu wouzira pawiripawiri ngati Mofolo. “Akafunefune ntchito kumene amalora wogwira nthito kuwiri pano sitingakwanitse kumasunga anthu achibwana amene sakhutira ndi malipiro awo.” Anapitiliza motero bwanayo mumkwiyo wakewo, panthawiyi n’kuti diso liri pantunda ngati watsinkha tsabola wa kambuzi. Ndi mawuwa zinadziwikiratu pa makonde amaofesiwo kuti msuzi udali utatha m’mbale mwa Mofolo ndithudi, yake inali itauma. Panalibe kumumvera chinsoni mkuluyo chifukwa anali atayikolosa dala yekha mbonawonayo. Zoonadi kudali koyenela kukhaulitsa chona mmodzi kusiyana ndi kuthetsa matemba a kampani yonse. Wokhawo achibwaana ndi amene akanachita mano je, kupichira ndudu za phwete kumkhalidwe wothothoka msidze ngati wa Mofolowo.

Anali dolo Mofolo pogwira ntchito kuwiri. Kwa iwo amene anapalana ubwezi ndi chilungamo, amkamudzudzula kuti mchitidwe wakewo siumkasiyana ndi ukawalala. Pofuna kudzipenta utoto woyera, amkayankha mosanthunthumira kuti amkapangako sikunali kuba chifukwa utambwaliwo amkapangira boma, “Kodi inu munamvapo kuti munthu waba ku bowa, mwapanga bwanji anthu wopenga? ” amkafunsatu fuso la munthu wina wotchuka Mofolo anthu akamupanikiza kumukhatamiza ndi Mvula ya malangizo.

Analidi tsotsi Mofolo. Amati mwezi ukamafika pakati, amauyatsa wa ku Dowa kukagwira ntchito ya za umoyo kwa sabata imodzi pachipatala china kumeneko. Ku ntchito kwinaku amapempha masiku atchuthi. Zimkamuyendera bwino mwezi ukatha, ankaliwona dziko likumumwetulira, kumuyamikira kuti anali mwana wochenjera. ndindani sakalumphalumpha ndi chimwemwe atakumanizana nawo mwayi wokang’antha a timba awiri ndi mwala umodzi?
Anabwatika mabwana ake kwa nthawi yayitali koma tsiku linakwana limene eni nyumba anagwira chona amene amkawatsinkhira matemba. Anagwidwadi Mofolo, la fote linamukwanira. Koma dzikoli n’lopusitsadi ndithu. Limakusekelera ukamapanga zombwambwaza koma likati likupunthe mbama, limatsotsombetsadi mopanda chinsoni. Zikafika pamenepa munthu amadziwa kuti Chibwana chimasisimitsa ndipo ngati mkotheka kuchipewa ndibwino wosazengeleza kutero. Mofolo ndi mboni ya zimenezi.

Linali tsiku loweruka. Ngakhale inali nthawi yozizira, Kadzuwa kadatuluka mokhulupirika. Kwa iwo amene analibe zochita zambiri m’mawa wa tsikulo, anachiwona chopambana kuwamba matupi awo ku kadzuwa kachikokako. Koma kwa anthu wotangwanika ndi ntchito za m’dziko, iyi inali nthawi yabwino yolunjika ku magalimoto. Kwa amene amapita ku ntchito pa njinga za kapalasa iyinso inali nthawi yabwino yopanga ubale ndi mitsegwede yawoyo. Tsoka kwa ofufuta nyerere, iyi inali nthawi yotukwanizana ndi zidendene zawo ulendo wa Abraham wokagwira ntchito ku malo osiyanasiyana. Monga anthu ena onse anali pikitipikiti kukonzekera maulendo wosiyanasiyana, bwana wa kuntchito kwa Mofolo wa ku Lilongwe analinso pa ulendo wopita ku Dowa kukazonda amayi ake amene amadwala mutu wa ching’alang’ala. Pa nthawiyi n’kuti Mofolo atapemphanso tchuthi ku ntchito kwake ku Lilongwe. Poti mayi wa bwanayo anamugoneka m’chipatala, sakanachitira mwina munthu wamkuluyo koma kulondola kuchipala komweko. Gululu! ! Anakampeza Mofolo atakangalika kugwira ntchito muchipinda mmene anagoneka mayi wa bwana uja. Atamuwona bwana wakeyo anangoti kukamwa kakasi Mofolo ngati wagwera m’lichero la nsima pa sadaka. Aname? Ayi. Panalibe bodza limene likamutsitsa pa ntandapo. Anali atamvala muja amamvalira anthu wogwira ntchito m’chipatala.

“Aaa! Chimenechi ndiye tchuthi chija eti? ” Anafunsa bwanayo. Ngakhale amkamwetulira, zoona zake n’zakuti mkati mwa chifuwa chake mumayaka moto. “Mukachoka kuno kubwelera ku Lilongwe mukandipeze ku Ofesi.” Analamula bwanayo. Ndindani akanatsutsa Pa nthawiyino mkuti tsinya litachita katambalale pa chipumi pake. Pa nthawi yoweluka mkulu wa pa chipatala cha pa Dowa pamene Mofolo amkagwirapo ntchito akanamizira kutenga tchuthi ku Lilongwe, anamuyitaniranso ku Ofesi. “Ndakuyitanani a Mofolo. Pa chipatala pano antchito achulukitsa, ndiye taganiza zochotsapo amene amangowoneka mwa apo ndi apo. Pepani kuti muli m’gulumo, kalata yokudziwitsani za kupumitsidwa ntchito kwanu ndi iyi.” Anatsindika mkulu wa pa chipatalapo kwinaku akupeleka kalata imene inanyamula uthenga wosautsawo kwa Mofolo. Analakalaka nthaka itamumeza Mofolo. Amkadziwiratu kuti nkhwangwa ina imkamudikira ku Lilongwe, mosakayikira konse ikamugabazula mopanda chinsoni monga inachitira ya ku Dowayo. Anadziwa mochedwa kuti mapanga awiri amvumbwitsa.

*Innocent Masina Nkhonyo
Chancellor College
P.O. Box 280
Zomba
09268999

< br>

SAVIMBI

Wolemba: Innocent Masina Nkhonyo*


Anthu amene anabwera kudzadzimvera wokha mtudzu wa Savimbi amkangopukusa mitu kulephera kukhulupirira zimene mapilikaniro awo amkatumiza ku ubongo. Panthawiyi n’kuti milomo ya Savimbi atayipinda ndi mwano wovuta kufotokoza. Kunena mosalambalala chichewa imkawoneka ngati mpindilo wa mphasa. “Ukadzayambiranso zopusazi ndidzakufafantha udzadziwa polekera” Analavula mphezi Savimbi kuwopseza mtsogolereri wa wophunzira wonse. Ngakhaletu Savimbi amkasanza mwano chotero zowona zake zinali zakuti woyenera kupepesa anali myeyo. Chifukwa cha kamtima kake kapena tinene kuti chimtima chake chodzitenga wozindikira pa chirichonse amangochita zinthu wosafunsira maganinzo, Analibe kulabadira zakusadziwa kwake pa zinthu zina. Mkhalidwe wopusawu unawonongetsa zinthu zambiri za sukulu komanso za wophunzira ena. Amkadziyesatu dolo Savimbi mnyamata wamtali ndi nkhope yomwe ngati msema zipande. Wamilomo yofiyilirako. Wakhungu lakuda, ayi koma loyererako akanakhala mango tikanati wowezukirapo. Nayenso anabwera pa sukulupo kudzafusa Mulungu ngati amkamuyitana kuntchito ya utumiki kapena kunali kuthedwa mzeru ndi kusowa kwa ntchito m’makukamu. Amkadziwa bwino zifukwa zake zopenzekera pamalopo anali Savimbi mwini wake. Ngakhale zifukwanzo amazidziwa yekha mkulu wodziwa zonseyo, ife timkadziwa kuti anali atalemba mayeso mukalasi lotsiriza ku Sekondale zilumika zingapo zapitanzo. Mphekesera zimkatipezanso kuti mkuluyu anapitanso ku Kasungu kukathandiza achikumbe akumeneko kulemera. Kupita ku famu inali njira yokhayo akanapezera mawisikoti amkavala pa sukulu ya tsopanoyi.
“Matengatenga woyang’anira za kuyitanidwa anakatenga chitedze.” Amkawuzana anyamata anzake akadutsana naye Savimbi. Ndi ndani pa sukulupo amene samkadziwa kuti Savimbi anali wakhalidwe lopotoka. Ena amkaganiza kuti kwawo anali Nyakwawa mkuluyo. Enanso amkaganiza kuti Savimbi anali munthu wabwino asanafike pa malopo koma kuti anamulakwitsa ndi agogo ake amenenso anathawa kusukulu yosulira atumiki yaying’ono. Pali mawumboni akuti gogoyo anawuza Savimbi kuti maphunziro azamzeru amafunika khama. Komano khamalo amanena ndi pa zopusa pomwe? Panalibe yankho loyenera limene likanaperekedwa pa moyo wa Savimbi.

Anabadwatu Zalowaapa Kaferekwanu. Pa sukulu yatsopanoyi analembetsa kuti dzina lake ndi Hippo Kant, amene akuwadziwa bwino mayinawa amkanena kuti Hippo ndi dera lina kumene kumachokera wazeru wina ndipo Kant linali dzina la abambo a wanzeru winanso. Komano n’chifukwa chiyani Savimbi anaganiza zotenga mayinawa kukhala ake? Mtudzu basi, anali wamtudzu mkuluyo. Komano dzina loti Savimbi linabwera osati chifukwa cha ndebvu ayi. dzinali linaperekedwa wophunzira ena atawona mofulumira zipatso za mkulu wa gulu la nkhondo logalukira ku Rwanda pa moyo wa Zalowaapa Kaferekwanu. Ngakhale mwini wake amadana nalo dzinalo ngati chilonda cha pa msana, sukulu yonse inagwirizana kuti panalibenso dzina lina limene likanaperekedwa kwa fwikinini ya munthu ngati Zalowaapa kuposa la Savimbilo. Linamukhala bwino dzinalo.
M’zochita zake, malankhulidwe ake ankafuna azikhala ngati wa ku Chilinde ku Lilongwe. Koma mawonekedwe ndi kavalidwe kake ka makedzana ndikamene kamkamuwulura kuti anali mbada yachabechabe, m’weta mphalabungu wa kwa Chitekesa mudzi wotsalira kwambiri m’boma la Phalombe. Kunene mosapsyatira analibe zifukwa zokwanira zotumbwira pa maso pa wophunzira wochokera m’matawuni.
Wophunzira azake atayesa njira zonse zomuthandizira Savimbi ndikulephera, anagwirizana zomusemera nyanga ya nsatsiyo kuti yimfotere yekha.

*********************************** **************************
Monga mwachizolowezi masana a tsiku lina wophunzira anatuluka mnyumba zawo. Inali nthawi yokamwa mtenthandemvu wopanda mperekezi. Pa chipata pa sukuluyi panayima kagulu ka azimayi ndi ana komanso makosana ena amene anabvala nkhope zokwiya kwambiri mipini anali atapachikira pa mapewa. Wophunzira anadziwiratu kuti panali patanunkha mphira pamalopo. Posakhalitsa zinadziwika pa sukulupo kuti wophunzira wina woperewera nzeru anachiwona chopambana kuwusira zilakolako za mthupi mwake pa kamtsikana kena kamene kanali pa chipatapo kulongosola mawonekedwe amkulu wosadzigwirayo. “Wamtali, wofiyira milomo komanso nkhope yake ndi yayitali” kanatero kamtsikanako. mkulongosolako aliyense anadziwiratu kuti anachita zachipongweyo sakanakhalanso wina kupatula Savimbi. Palibe anadabwa ndi khalidwe la Savimbi anali atawonetsa kale chidwi pa ntchito ya mdimayi mkachisi. Tsoka ilo amkafuna kupanga zachipongwezo kwa buthu la ku Mangalande limene silinawonetse dzino kumchitidwe wosusukawo. Uthenga unatumizidwa kukayitana Hippo Kant. Sanawilingule analibe mwayi wosankha kupita kapena wosapita chifukwatu amkayitanayu anali m’modzi wa Asuli pa sukulupo. Atafika pa chipatapo aliyense anadziyamikira kuti anapambana polumikiza malongosoledwe amwanayo ndi mawonekedwe a Savimbi, Panalibe kukayika kulikonse, anadya gondolosi kwambiriyo anali Savimbi, Hippo Kant. Nkhani inavuta, atakambirana ndithu kwa kanthawi makolo amwanayo ndi asuliwo panaperekedwa nkhope za John Chilembwe mwachinsinsi. Sipanapite nthawi yayitali kuti galimoto ilire, analamulidwa Savimbi kuti akwere. Analonjezedwa kuti katundu wake amubweretsera cha tsiku linalo. Ndi wosula wuti akanalora munthu wowononga ngati Savimbi kuchita pondupondu pa malo woyerawo m’dzina lolongeza katundu.

Patapita miyezi isanu chichokereni Savimbi, kunayamba kumveka mphekesera kuti Savimbiyo anayamba kupota tsitsi. Wophunzira amene amkachokera kudera la kwawo anadzafotokoza akuchokera ku tchuthi cha Pasaka kuti mkuluyo anayamba kuvula kabudula m’malo woyenera ndikumamubvala m’mutu kenaka amagundika kusekerera mitengo ya mapeyala. Wophunzira ena atamva za nkhaniyi anamva chinsoni. Anadziwiratu tanthaunzo la zonsenzo sanasowekenso kuwuzidwa za tsogolo la Savimbi.

*Innocent Masina Nkhonyo
Chancellor College
P.O. Box 280
Zomba
09268999ZOONA ATSIBWENI?

WOLEMBA: Innocent Masina Nkhonyo
Anagudubuka mokodola ngalawa zachinsoni pa kama m’chipatala Zagwazatha amene mwachidule amkangomuyitana kuti Zagwa. Ukutu kunali kuzuzika ndi ululu wa mankhwala ena wokhethemulira moyo wotchedwa Tameki. Aliyense amene anatchethukira ku chipatalako kudzadziwonera ndi kudzadzimvera chimene chinamuchitikira Zagwa anali pefupefu pa chitseko chachipinda mmene anagonekamo Zagwazatha. Palibe amene anamulora kuchita chipumi dzeka mchipindamo. Mumayenera kukhala achipatala wokha basi. Kwa iwo amene amakondwa ndi kupeka nkhani, ili lidali danga lotchezera chidulo cha bodza. “Iii! Angodikiratu kuti atsirizike, tikakamba za moyo ndiye wa nkhuku bolanso watalika.” Amkakokomeza za mtanda umene anaseza Zagwa anthu wosamufunira zabwino. “Kodi mukuti anamulanda amene akanazakhala alamu athu kutsogolo kuno? ” Nawo mafunso okolosa mayankho a bodza amkavumbulutsidwa. “Ayi koma kuti amupeza nako ndiye amafuna asazuzike kwambiri.” Amkaperekedwa mayankho ngakhale woyankhawo anali anthu wosamudziwa Zagwazatha. Zimene anthu ambiri amkakamba zinali zongopeka kufuna kukometsa mabvutowo, ndi angati amene amakondwera wina zikamamuyendera bwino? Anthuwa mosakayika konse amakondwera ndi tsoka limene linamugwera Zagwa.

Womudziwa bwino mnyamatayo anali ndi maganizo wosiyana. Kwa iwo iyi inali nkhani yobvetsa chinsoni. Ambiri amkagwedeza mitu kwinaku akudziguguda pa zifuwa. “Mnyamatayu wazuzika kale kwambiri, n’chifukwa chiyani Mulungu walora kuti azuzikebe moposera apo? ” anthu amkafusa mafunso wodzudzura chilungamo cha Mphambe, Mulungu wa Yobu, wolanga anthu wosalakwa m’dzina lowayesa. Tili pa mdipiti mthengo la maganizo ndi manong’onong’o wosiyanasiyana pa zatsoka limene linazuzunda chipumi cha Zagwa, pamalopo panafika mayi wina wa chikulire. Mayiyo amkasisima ndipo songa za kachitambaya kamene anavala zimkayamwa misozi imene imkatsikilira mmasaya wokwinyika agogoyo.

Chinsoni chinatigwira wosati chifukwa cha Zagwazatha ayi koma mmene amkaonekera mayiyo. Zovala zimene anavala zinali zachidziwikire kuti mayiyo anali atathambitsidwa ndi mapama a mdani uja wotchedwa umphawi. Anatipatsa moni wa pa dzanja mayiyo ndipo ena mwa ife amene analandira moniyo anayamba kuyang’ana m’manja mwawo mwa chidwi. Inenso ndinayang’ana mwanga. Ndimkayembekezera kuona m’manjamo mutakandika. Ndi mwana uti wa mtauni amene sakanalira atagwiridwa ndi manja a mayiyo. Analitu manja wokhakhalala moti kukuphaphalitsa nalo bwande ungathe kupepe uli chogwada kuti sudzayambiranso. Ichitu chinali chidziwitso choti mayiyo anali pa ubwezi wa ponda apa nane mpondepo ndi khasu. Ngakhale mawonekedwe agogoyo samkatilora kuganiza zoti gogoyo angalime, komabe akanatani poti kulima ndi njira yokhayo yokhalira moyo kumudzi.

Kenaka nthawi ya tidziwane inakwana ndipo tinamvanso chinsoni titauzidwa kuti mayiyo anali mayi wa Zagwazatha. Nawo anabwera monga kholo kudzadzionera wokha chimene chidamuonekera mwana wawo.

Tili mkati momvetsera malonje a mayiyo pamalopo panafika njonda ina yowonetsa kuti ndalama zimamumvera akaziyitana. Ngakhale mkuluyo anavala buluku lofupikirapo palibe akanakayikira kuti njondayo inali khumutcha. Mkuluyu anabweranso ndi zolinga zake koma osati kudzaona Lazaro wachabechabe ngati Zagwazatha. Umutu ndi mmene timkaganizira komatu mawu amene anatulutsa gogo uja anatitsutsa. “Zoona achimwene nanunso mumabwera kuno, simukananditenga nanga pa galimoto yanuyi? ” Umutu ndi mmne anadandaulira mayiyo. Tinadziwa kuti anthuwo amadziwana. Kupatula kudziwana chabe nkhope za awiriwo zimafananiranapo. Sizinatitengere nthawi yayitali kuti tidziwe kuti anthuwo anali pa chibale. Njonda inabwerayi inali mng’ono wa amayi a Zagwazatha ndipo inali mzime m’banja lawolo.

Pakanapanda awiriwo kubwera, chitseko cha chipinda chimene anagonekamo Zagwa sichikanatsekulidwa. Anapatsidwa mwayi awiriwo kulowa ndipo ine ndi kujijirika kwangaku, ndinalowa nawo pakhomo lophaphatizalo. “N’chiyani mwana wanga, umafuna kudzipheranji? ! ” Inalira zenizeni ntchembere ija.

Panthawiyi mkuti a malume ake a Zagwazatha amene dzina lawo amawati a Mofolo akuyang’anitsitsa Zagwa osati mwa chinsoni koma mokwiya kwambiri. “Adotolo munthu akuzuzika uyu tangomalizani.” Tinamumva malume uja akuwuza dotolo m’maso muli gwaa. “ayi a chimwene yekhayu ndisiyileni.” Uyu anali mayi uja kudzudzula maganizowo. Chinachake chowopsa koma chachinsinsi chinali chitachitika kuti Zagwazatha afike pamenepa. “inu a chimwene ndinu munthu woyipa kwambiri. Muyambeno kutsinkha ana anu a ine akukwanani.” Uyutu analinso mayi uja kulankhula mwa andifinyeandifinye. Ine monga mtolankhani wolowera mkalasi sindinasowekerenso kuti mayiyo apitirinze kufotokoza kuti ndidziwe chimene chinachitika. Aliyense mchipindamo anadziwa kuti a Mofolo, a tsibweni a Zagwa, amafuna kukhwimira chuma chawo popereka nsembe moyo wa Zagwazatha. Zoti Zagwa anamwa Tameki zinali zoona koma ichi chinali chiphimbam’maso chabe. Ng’anga imene inalongosola zonsezo inapepetula Zagwazatha kuti amwe Tameki m’matsenga n’cholinga choti anthu aziti wadzipha koma moyo wa Zagwa atatenga kale.

Anthu anayamba kutuluka mchipindamo moyipidwa kwambiri. Amene anatulukawo amakanong’oneza azawo panja zoona zenizeni zimene zinachitika kuti Zagwazatha amwe Tameki. Sindinadabwe nditaona njonda zokhulupirika zikusonkhanitsa miyala, zilemba za mkwiyo zili pa zipumi. Thukuta linatuluka pa nkhope ya atsibweni a Zagwazatha. Ndikhulupilira amkadziwa kuti miyalayo imadikira iwowo. Inenso zoti ndine mtolankhani ndinayiwala. Monga munthu wina aliyense, ndinali ndi ulemu wa ukulu pa mphatso ya moyo. Sindikanasekelera anthu ankhalwe ngati atsibweni a Zagwazatha kumaseweretsa miyoyo. N’chifuka chake lero lino sindimadandaula kuti ndinayambitsa mwambo wolanga mfitiyo ndi ine nditayikwapula mapama wowonetsa nyenyezi mchipinda momwemuja. Titatulutsa mkulu wodzikondayo panja zimene aliyense okonda moyo amayembekezera kuti zichitika zinachitikadi. Kunali kupamantha, kupumuntha ndi kuponderedza……………..
Nthawi imene a polisi amabwera n’kuti ife mbali yathu ngati zika zolemekeza moyo titachita kale.

Innocent Masina Nkhonyo
P.O. Box 280
Zomba< br>

ATAMBWALI SAMETANA

WOLEMBA: Innocent Masina Nkhonyo*

“Usonkhanitse tiakatundu tako tonse ndikhulupilira kuti njira yakwanu ukuyikumbukira pano uchokepo. Sindimafuna kumandidoda ngati mpira wa chikulunga ine.” Nkhope ya Kalimwini inali itadzola mafuta wotchedwa ukali pamene amkanena izi. Panthawiyi nkuti milomo yake ikunjenjemera ngati ikuvina gule wa Ndombolo. Nawo maso ake anali tuzuu pantunda ngati watsekedwa pakamwa ndi mbatata ya Kamchiputu. Mkazi wa Kalimwini, Nagilemba, anali njenjenje chapotero. Amkadziwa bwino chimene chikanamuchitikira akanayandikira mkango umkabangulawo. Panthawiyi n’kuti kakhanda kanadzetsa mpungwepungwewo kakulira mokokomeza kumbuyo kwa Nagilemba ngati kagwera pamoto. “Ndati utute saza zako hule lachabechabe, kamwana kakoko ukapatse chitsiru chako umapanga nacho zo…….”sanamalize chiganizocho Kalimwini, ukali unapangitsa lilime lake kuti lilemera m’kamwa ngati galoni ya deneka. “Mwana siwayine uyu! ” Amanena izi aku akulunjika kumene kunaima mkazi wake. Zoonadi mwanayo analibe chizindikiro ngakhale chimodzi chosonyeza kuti bambo wake anali Kalimwiniyo. Monga mwamuna wina aliyense wanzeru zakuya, anali ndi zifukwa zokwanira Kalimwini zodabwira mawonekedwe akhandalo limene limakwanitsano miyezi itatu chibadwireni m’banjamo. “Chichitikechichitike koma ine undiuza zoona, kupanda kutero lero uwatsatira ambuyako kunkhadze. Wandidyera zambili hule” amanena izi akufinya dzolimba pakhosi pa mkazi wake ndi dzanja limodzi ndipo linalo amaponya zibakera mwamkaziyo ngati akuwomba nyemba za phalombe kuzichotsa mmakoko ake. Mzowonadi anali atamanga fundo yakeyo Kalimwini. Akakumbukira zambiri zimene mkazi wakeyo anamudyera samaonanso chifukwa choti mkazi wosayamikayo akhalirenso ndi moyo. “Ta-ndisiyani- kay-e ndin-en-e zo-ooon-a” anachondelera koma mobanika kwambiri Nagilemba, kumpempha mwamuna wakeyo kuti amusiyire moyo.
“Nena msanga! Mfiti yosayamika.” Analamula Kalimwini kwinaku akuchotsa dzanja lake pakhosi pa Nagilemba kuti awulure koma zibakera zimapitilira kutera pathupi pa mkaziyo. “Anandilakwitsa ndi a Tengelepena. Mwa-mwan-ayu ndi-ndi-wawo.” Ananena tchutchutchu Nagilemba. Akanatani mwana wamkazi akuchita kuyiona imfa ikubwera chapoteropo. Amayenera kunena chilungamo kuti apulumutse moyo wake wokondeka. “Chani? ! Tengelepena? ? Zosatheka! Tiye komweko.” Ngakhale Kalimwini amawoneka wodabwa ndi kutchulidwa kwa dzina la Tengelepena samayenera kutero chifukwa anthu ena womukonda anali atamuunikirapo kuti khandalo limafanana kwambiri ndi Tengelepena, mzake wa Kalimwini wa ponda apa nane mpondepo. “Tiye komweko! Ikandimva madzi nkhanu iyimeneyi” Anatsogozana ulendo wa kunyumba ya Tengelepena. Sipanali patali kwambiri choncho sizinawatengele mphindi zambiri kufika panyumbapo. Zimene anakakumana nanzo pakhomopo, zinapangitsa kuti zochitika zonsezo zikhale ngati filimu ya ku Nigeria. Kunyumba kwa Tengelepena kunalinso chipwirikiti. Naye Tengelepena anayitulukira kuti mkazi wake amamuyenda njomba. Inaulura zonse ndi kalata imene inapezeka mthumba la siketi ya mkazi wa Tengelepena. “Eya! Wachita bwino kubwera khakhakha, utenge chidole chako muno ndi hule lakoli” Anakalipa Tengelepena kwinaku diso lake la nkwezule atalibzala pa nkhope ya Kalimwini. Akanakhala maloto zochitikazo, wolotayo akanalakalaka wosagalamuka kutuloko kuti azingomvabe kukoma kwa malotowo. “tawerenga zimene unalembazi mbutuma” anakana kuwerenga kalatayo Kalimwini. Amkayidziwa bwino tsemwe linamugwira Kalimwini. Anadziwa kuti yakenso yapheduka. “Chitsiru chakana kuwerenga anthu inu ndithandizeni kuwerenga” uyu anali Tengelepena kupereka kalatayo kwa anthu amene anabwera kudzawonelera filimuyo. Inawerengedwadi kalatayo.

Wokondeka mngelo wanga,
Choyamba ilandire moni nyenyezi yanga imene indikodolera zisangalalo zokhumba mtima wanga. Madandawulo ako ndamva.mwanayo ndizimuthandiza. Sindingalore kuti Kaliveni amene ali magazi anga enieni adzivutika bambo ake ndili moyo. Ndikulonjeza kuti ndizimuthandiza koma mosamala kwambiri. Chonde upitilize kusunga chisisi chimene wakhala ukusungachi kwa nthawi yayitali.
Ndatha ine wakowako amene mwini chilengedwe anakupatsa.

Kalimwini.

Anthu anawomba m’manja kalatayo itawelengedwa. Analibe ngakhale mwayi wokana Kalimwini, zoti manja anakhwakhwaza zilembozo anali ake. Aliyense pamolipo amkazidziwanso bwino zimenezi. Zinadziwika kuti naye Kalimwini amkazemberana ndi mkazi wa Tengelepena. Naye Kalimveni anawadziwa abambo ake enieni patsikuli. Chinali chimvumbulutso chimene chinasiya anthu ambiri akugwedeza mitu. Pa zimene zinachitikazo ndindani amene sakanalingalira kawiri katatu ndikupichira ndudu yotchedwa mseko wachikhakhali cha mano jeee za zimene zinachitikanzo. Anthutu amkaseka kuti chikondi cha awiriwo chinafika pandime ya nyambita apa nane n’nyambitepo. Anayang’anana amuna awiriwo kwakanthawi moto waukali ukulilima m’maso mwawo. Analibe zifukwa zoweruzira akazi awo. Anali amuna wosakhulupirika. Ngakhale panalibe zifukwa choponyerana zibakera komabe tsogolo chi ambwana, cha amuna awiriwo linali litaulutsidwa ndi mphepo ya chimvumbulutsocho. Anthu amene anabwera kudzawonelera zochitikazo amkabwelera m’makomo mwawo akutsimikizirana kuti akulu akale sanali wopenga ponena kuti atambwali sametana, analinga atawona.

*Innocent Masina Nkhonyo
Chancellor College
P.O. Box 280
Zomba
< br>
NDINAPEZEKA BWANJI MUNO

Wolemba: Innocent Masina Nkhonyo

“Titembenuke! ! Ndati titembenuke Mbutuma inu! ” Kunali kubangula kwa agalu psatirani michira kuchokera kwa Motokosi mbadwa komanso mfumu ya m’chipinda chathu cholandiliramo malipiro pa ntchito za mdima zimene tinali titagwira tili kunja kwa chipindacho. Phuu! phuu! phwaa! ! ! “Mdala tafulumira wangoti ndwii ngati wameza njinga bwanji? Siunamve zoti tikembenuke? ! ” Analirimanso wina ngati njoka ya Songo yopemeleredwa ndi utsi ku una. Amageya ntudzuwo atawapulumutsa kale makofi wowonetsa zithwanithwani. “Pepani bwana kungoti mbali tikutembenukirayi nyamakazi ukumandipweteka kwambiri ndiye ndikufuna kumayinyengelera kuti mwinamwake ndichepetseko ululu” Kanayankha mokodola chinsoni kankhalamba kamene kamkakhatamizidwa ndi mapamako. Ndinamva chinsoni. “Nyamakaziyo ndiye chiyani? Muli akazi muno? ! Umfiti eti? Tatembenuka mdala! ! ! ” sindinalabadirenso zandemangayo. Ndinadziwa kuti zinalowa chibwana. Ndindani wa nsinkhu wathu m’chipindamo akanalifefetula bodza kuti sadziwa nyamakazi?

Fungo limene limkachezera mwasangala makonde a mphuno zathu limkatikumbutsa za milandu yosiyanasiyana imene tinapalamula kuti tipezeke malo a mdimawo, ndende. Munalitu phokoso lakukhosomola ngati ena atsinkha tsabola wa kamphiripiri mwa ngozi. Munalinso kutentha m’katimo kumene kumkapangitsa enafe kuganiza kuti tinali mbobo za chimanga m’chiwaya chokazingira. Ndikanena za kuyabwa m’chipindamo ndiye phokonso limene limkamveka njonda zikafatsa kukanda kuti kekeke, lingathe kundiyikira umboni. Kwa iwo amene amakhalako motakasuka mkatimo amapezako mwayi woswa nsabwe zimene zimafuna kumasandutsa matupi awo phwando la sadaka. Tikakhala enafe ngakhale kukanda timkakukhumba, kuthithikizana kwathu sikumatilora ngakhale kutambasula manja ndi kulanga nsabwe zadyeranzo pozithudzula ndi kuseri kwa zala zathu. Tinkamva kuwawadi nsabwezo zikayamba kuyamwa magazi athu koma palibe chimene tikanachita, timangozilora basi kuti zikhale anzathu womakamba nawo nthano m’dziko la zowawalo. Ngakhale zikope zathu zimafooka n’kutuzula maso panalibe mwayi wopha tulo. Mikonono imene imkamveka m’chipindamo inali ya a nyapala wokhawo amene anazolowera moyo wovuta kusimbawo.

“Eee fwee fwee! Eya ayise tikumana mawa ku tharaveni. Eya tikamwera zako fwee khekhelereee.” Uyu anali mnyapala wina kubwebweta kutulo. Ndinamumvera chinsoni. Ndimkadziwa kuti ku tharaveni amkati akakumana ndi mzakeko sakakumana, akanakakumana bwanji ali mkayidi? Zinali zachidziwikiretu kuti mawa amkanenalo tidzadyera limodzi nyemba za anamkafumbwe. Maloto pena amapusitsadi inu, amakufikitsa kumene zidendene zako sizingapondeko.

Ndili mkati molingalira za kubwebwetako wina anakhosomola mwa ulamuliro. Ndinakhala tcheru chifukwa ndinadziwa kuti panali mawu, zoonadi inali ndi mawu mfumu yathu Motokosi.
“Timverane abale anga amene dziko linatiponya muno kuti timve zowawa. Monga mwa chizolow……..” Anadukiza kaye Motokosi atazindikira kuti ena amalizabe mikonono. Analamula kuti amkagonawo agunyuzidwe. Tinawaona wokonda tulowo ali maso phethiphethi modabwa, kenaka kudabwako kunachoka atazindikira amene amalankhula panthawiyo. “Monga mwachizolowezi usiku uno ena mwa azathu atifotokozera chimene chinawachotsetsa m’dziko la mkaka ndi uchi.” Uyu anali Motokosi kupitiriza.

Anayamba kusanthula mbiri yake usikuwo anali Kadziwotche, munthu wosanthunthumira povumbulutsa za kukhosi. “Zoonadi abale anga nanenso ndili nazo zifukwa zimene zinandibweretsa kuno. Ngakhale ambiri simukhulupilira komabe ndibwino kuti mudziwe.” Ndinaona makosi akaidi amzanga ali sololoke kufuna kudziwa mbonawona imene inakokera Ndomboleni kumalo amasautsowo. “Ndinali mmodzi mwa aphunzitsi pa sukulu ina m’mzindamu. Kuti ndipezeke muno ndichifukwa choti ndinakanitsitsa kwantu wa galu ndi kunena poyera zoti mkulu wina amene ankafuna kuyimanso pa mpando wina asayimenso.” Anthu m’chipindamo anayang’anana modabwa. N’zachidziwikire kuti anthuwo samkapeza chifukwa chenicheni chimene chinabweretsa mzawoyo kumalowo. Kunena kuti ‘sayimanso’ sichinali chifukwa chokwanira. Kenaka anapitiriza Ndomboleni. “Ndiyetu anandiponya muno pondiganizira kuti ndinakamba zinthu zoti zingathe kuyambitsa chisokonezo. Papita zaka zisanu tsopano koma sindinaweluzidwebe m’bwalo la milandu.” Tinamva chisoni ndi nkhani ya mzathuyo, panalibe chifukwa chomuponyera m’malo wozuzawo. Kukhala akaidi sikumatipangitsa kuti tisadziwe chilungamo, apatu panalibe chilungamo. Zaka zisanu mkayidi wosaweluzidwa pankhaninso zopusa?

Atamaliza Ndomboleni kufotokoza mbali yake, inafika nthawi ya Lapukeni. “Ine akuluakulu ndinapezeka muno chifukwa choti ndinadya gondolosi kwambiri.” Munali kuseka m’chipindamo, phwete lathu linatiyiwalitsa kuti tinali akayidi. Kodi dzikoli likupita kuti, zoona ayamba kumanga ndi wodya gondolosi womwe? Ilitu linali funso limene timkadzifunsa titamva tchimo la Lapukeni. “Fotseki! Iwe Lapukeni chibwana ayi, sinthawitu ya nthano ino. Kudya gondolosi sangakumange nako, tiwunze zoona ambwana” uyu anali Motokosi kufuna kudziwa zenizeni diso liri pamtunda. “Zoonadi akuluakulu ineyo ndinabwera kuno chifukwa cha gondolosii… ayi koma kuti ndinagwililira.” Sitinamumvere chinsoni mkufotokoza kwa chiwiriko. Wogwilira amayeneradi kulangidwa, panalibe chifukwa chonamizira gondolosi.

Titamaliza kumva nkhani za gondolosi ndi kugwililira, inafika nthawi yanga yofunthula za momwe ndinapezekera m’chipindamo. “ Akuluakulu ine ndine konsitabo Potolani.” Ndinayamba motero. “Ndinali wa polisi wolimbikira ntchito ndithu moti mbamva, wogwililira, wosuta kanundu, wosunga mapikitchala wolaula ndi akatangale ndakhalapo ndikukwidzinga ndi unyolo.” Ngakhale ndinaona pa nkhope pa akaidi ena patalembedwa zilembo za mkwiyo, ndinapitiriza kufotokozako mwamatama.
“Ndiye ndikupezeka muno chifukwa choti tsiku lina ndikubalalitsa anthu pa zipolowe, ndinawombera mmodzi mwa iwo mwa ngozi. Panopa ndikudikira kuzengedwa mlandu wakupha.” Nditangoliza umboni wangawo ndinazindikira koma mochedwa kwambiri kuti mbiriyo ndinayikamba malo wolakwika. Ena mwa akaidi amzangawo anali atalawako unyolo wowakwidzinga ndi manja angawa. Sindinadabwe nditamva wina akukuwa kuti, “uyu si mzathu! ! ” anandiundilira akaidi azangawo, ndiyetu kunali kunditekesa, kundipamantha, kundiumbudza ndi kundifafanthiratu……………………….

Chimene chinachitika potsatira kuphuvumulidwako sindikuchidziwa. Zimene ndikudziwa ndi zoti ndili m’chipatala; andimanga ma bandeji; mkamwamu mano wokwana asanu ndi awiri akusowamo ndipo a dotolo andiuza kuti ndizokayikitsa ngati ndidzagwiritsenso ntchito miyendo yanga. Zoti ndabwera bwanji mchipatala muno akudziwa ndi Motokosi ndi anthu ake m’chipinda chamazuzo chija.


*Innocent Masina Nkhonyo
Chancellor College
P.O. Box 280
Zomba
09268999
< br>TINKANENA

Wolemba: Innocent Masina Nkhonyo*

“Achimwene tamamveraniko malangizo. Anzanu mumayenda nawowo alibe tsogolo ngakhale lotchova njinga.” Anachondelera a Nankosi mphepo yaukali itachita katambalale pa nkhope yawo. Ndindani akanasekelera kuti Kolodiyo mnyamata amene anali atangomaliza kutsinkha nzeru zakuya ku Yunivesite kuti adziyenda ndi a bolamoyo osuta chamba ndi wobwira jang’ala ngati Lapukeni ndi anzake. Amkanena zoona mayiyo. Lapukeni ndi anzake analibedi tsogolo, amayendera Yobu 13: 13; chichitike chichitike. Akapita kuchipangano cha tsopano analinso ndipothawira; amalimbitsana mitima ndi pemphero la Ambuye, “mutipatse ife lero chakudya chathu cha lero, cha mawa tichiwona mawa lomwero.” Zinalitu fwikinini zosafunika kuyenda ndi munthu wopapira buku ngati Kolodiyo.

“Inetu ndimangoyenda nawo anyamata amenewa chemwali, sindipanga nawo zoyipa zawozo.” Anayensa kudzitsitsa pa mtanda Kolodiyo. “kaya, izo ndi zanu achimwene zidzatipeza, mwakula mwatha.” Anamusambira m’manja chemwali wakewo. A Nankosi sanakhalitse pamalopo kumalimbana ndi mlongo wawoyo, anali ndi zochita zambiri monga kuvuwula mphale. Anayifumbula ndawala ya bwino adona mundipondera mum’phika ulendo wokabwereka mphasa kwa anzawo a Nampuzeni.

Anthu amadabwa naye Kolodiyo, n’chifukwa chiyani amkayenda ndi kagulu kosiyaniranatu ndi maphunziro komanso zochita zake. Amkayankha mwachidule, “ Anzangawatu ndinadziwana nawo ku pulayimale choncho sindingawataye lero.” Ngakhale amvula zakale anamubenthulirako kuti Kalongonda saphikira limodzi ndi Mphalabungu, sizinaphule kanthu. Anapitiliza kuyenda nawo. Kwa nthawi yayitali anapewadi zochita zawo. Ngati iwowo amamwa mowa, myeyo amamwa fanta, komatu linafika tsiku limene anafuna atawonetsa udolo.

Mwachizolowezi ananyamuka ndi anzake opulukirawo nakalowa m’nkhalango ina. Zifukwa zolowera m’nkhalangomo amkadziwa ndi Tobiyansi mkulu wa gululo. Atafika pakabwalo kena m’nkhalangomo, anaganiza zochitira macheza awo pamenepo. Ndudu za fodya wamkulu zinayatsidwa. Wodziwa magwiridwe ndi makokedwe a katunduyo amkalandizana mwasangala. Pa nthawiyi n’kuti Kolodiyo akukhaphwira madzi azivwende za m’tchire. Anzakewo amkamudziwa bwino kuti anali apongozi ndi fodya wamkuluyo.
Patapita kanthawi, pamalopo panafika abuthu ovala modzumitsa ngakhale Lusifala. Akanakhala Anjelo anali nawo pa malopo ndithu akanalira ndi mavalidwe opotokawo. “Zoona adolo ngati inu mogoyi simumaphafa? Sikankhotakotatu aka sikakujudula kwambiri.” Anatero mtsikana wina. Sanayankhe Kolodiyo. ‘Ndikane? Ndiwoneka kape. Ndivomere? Akandikalipira koopsa chemwali aja akakandidziwa.’ Mosaganizira bwino analandira nduduyo kwa buthulo. Pofuna kuwonetsa udolo, anakoka chambacho mosasamala. Atamaliza nduduyo sanafunse ngati anali wololedwa kuyatsanso ina. Pamene amkamaliza ndudu yachiwiri anawona ngati dziko likuvina ndombolo amkawawona mozondoka.

Chotsatira chake sanamvetse. Anali m’chipatala. Anadziwona nkhope pa kalirole limene linali pafupi, anayensa akulota. Anali atatupa mochititsa mantha. M’mphechepeche mwake amkava ululu ngati wathotholedwa zimene simamuyeneleza kukhala mwamuna. Anapempha Mulungu kuti ampatse mphamvu zofunsira chimene chinamuchitikira. Anapezekadi wachifundo. “inutu munasuta chamba kwambiri. Atsikana amene munali nawo anakugwililirani atawona kuti mwabayizika, ndipo akupatsirani matenda aja a chindoko. Chifukwa chosazindikira munakakolosa njuchi zimene zakubabadani mopanda chinsoni. Pepani kuti a Polisiwa akukudikirani kuti mukatuluka muno mukayankhe mlandu wopezeka ndi chamba.” Anamufotokozera mwachindunji Kolodiyo. Anafuna kulira koma anamuletsa, anakumbukira kuti tinkanena anathera m’siizi.

*Innocent Masina Nkhonyo
Chancellor College
P.O. Box 280
Zomba
09268999< br>DEMONI WOTCHEDWA YAMIKANI

Wolemba: Innocent Masina Nkhonyo*

Ndinadzambatuka pa mpando umene ndinakhala m’kachisimo ngati galu watsoka wopwanthamulidwa khofi ndi nyani wolusa ku uzimba. Ngakhale ndinabvumbuluka ngati katumbu wotsotsombetsedwa pa mbuto ndi ndodo yotchedwa banya, sindinaonetse zizindikiro za kumene ndinkafuna kulowera pa nthawiyo. Ndinamwaza maso anga pa nkhope za anthu m’kachisimo ndili chiyimile komatu ndikunjenjemera ngati chithumwa cha sing’anga wothana ndi athakati. Ndikanadziwa kuti maso a anthu onse amene anabwera kudzanyogodola satana m’kachisimo akhodzokera pa ine, sindikanayelekeza dala kuyimilira. Ndinaona akuluakulu ena akunong’onezana chapoteropo. Ndinadziwiratu kuti ankakambirana zoti andikwidzinge ndi zingwe poti zimene ndimkapanga nditangokumva umboni wa Yamikani zinali zifukwa zokwanira zokapezekera pa chipatala china cha anthu amzeru kwambiri ku Zomba. Ndindani akanakayikira kuti ziwala zinali zitayamba kuvina gule wa Mbotosha m’maso mwanga? Ngakhale anthu wodzapereka mathungwa achiyamiko kwa Chautawo anali ndi maganizo woti ndaduka mzengo, mwiniwakene ndimkadziwa kuti sichinali chiyambi cha misala. Zoona zake n’zakuti umboni wa Yamikani, mkazi yekhayo amene ndinamukhuthulira chikhulupiro changa chonse, unali utalasa mtima wanga. Zimene ndimkapangazo kunali kulephera kuvomereza zoona za umboniwo. Ngakhale ndimkadzichedwetsa kuvomera za umboni wosautsawo, ndinalibe mwayi wosankha. Zoona zake ndi zimene ananena msungwana wangayo Yamikani, nkhawena ya munthu, ndulu ya ng’ona, njoka muudzu, mfalisi wa chinyengo. Andikhululukire Mulungu wa Abraham chifukwa cha mayinawa koma mtima wanga woswekawu siwokozeka kukamba zabwino za Yamikani, mtsikana amene wandikumbira dzenje. Ndikamamaliza kusakatula masamba wofotokoza za ubwezi wanga ndi Yamikani mutsimikiza kuti mayina ndatchulawa ndiwomuyenera demoni ameneyu ndiponso muwonjezera ena pa amene alipo kalewa.

Ndinadziwana nayetu mtsikanayu, Yamikani pa nkhani za mayimbidwe. Anali m’kwaya imene imkatsitsimutsa anthu pa Tchalichi chathu cha Kapuso. Inenso ndinali m’kwaya yomweyo. Chikoka changa mwa mtsikanayo chitafika pa ndime yakuya sindinachedwa kutulutsa Chichewa chimene mamuna wina aliyense akanatulutsa kwa namwali wothwanima moyiwalitsa mikwingwilima ndi zitopotopo za m’dzikoli ngati Yamikani. Ngakhale anayamba wandigubitsako kwa timasiku ndithu anavomera kugwa m’chikondi nane.

Mbiri ya msungwana wangayu aliyense amkalalika kuyambira kumudzi kwawo ku Umodzi kudzamalizira patchalichipo. Kukakhala zochitika za kumpingo Yamikani amkapezeka kutsogolo kuyendetsa dongosolo lonse la miyambo ya uzimu. Atamandike chiumbiumbi Mulungu mwini chilengedwe chifukwa cha mphatso ya Yamikani, ilitu linali pemphero limene silimkatalikira makonde a mtima wanga.. sindimkachita manyazi kuwuza anzanga a m’mudzi wathu wa a Chikang’a kuti Yamikani adzakhala mayi wa ana anga.

Timkakondana mokolosa nsanje m’mitima ya mbeta komanso anyamata ambiri a mphala. Chikondi chathu chinali chomwera m’kapu imodzi chija cha sipa nane ndisipeko. Ndinamukhulupilira kwambiri Yamikani chifukwa tikakamba za asungwana angwiro m’dera lathu mfumukazi yawo inali duwa langali. Samkaopa kulangiza apuludzu wothothoka msidze, zimbayambaya ndi agong’oli wosowa mkhalidwe. Ambiritu anatembenuka chifukwa cha upangiri wa nyenyezi yanga Yamikani. Nanenso ngakhale anthu akwathu, Angoni, amalemekeza kachakumwa ka tsoo, ndinathetsa ubwezi wanga ndi mbiya ya Gamazula. Sindimkafuna kukhumudwitsa mnjelo wangayu, Yamikani.

Kuyezetsa magazi ndi bwezi lako ndi chinthu chimene masiku wowopsa ngati ano aliyense amalemekeza koma pakati pa ine ndi Yamikani panalibe chikayiko. Ngati ndinkhani yokayikiridwa, anali wokayikitsa ndi ine mwa awirife. Komatu naye Yamikani ananditsimikizira kuti samandikayikira choncho samaona chifukwa choti tikayezetsere magazi. Ngakhale zinali choncho chikhumbokhumbo choyezetsa magazi chibwezi chathu chisanafike potengerana kumayesero chimandipeza pafupipafupi. Sindimafuna kupereka matenda kwa bwezi langa choncho ndinakayezetsa magazi anga mwa mseri tisanayambe kugonana. Zotsatira zinali zosangalatsa, ndinalibe achikulilewo m’magazi anga. Izitu ndizimene ndimkayembekezera, ndimkakhulupilira kuti ngati ndili nako ndiye kuti ndinakatengera ku nsima chifukwa ngakhale poyamba ndimamwa kachakumwa, pa nkhani zotengerana m’gombezazi ndinali munthu wodzisunga. Nditadziwa zotsatira zanga tinayamba kupanga zonse zimene mwamuna ndi mkazi wokondana amachita kuphatikiza kufunditsana gombeza limodzi. Tinapitiriza kuyenda m’njira ya chikondi ndipo malingaliro wodzamangitsa woyera amkachita adodolido m’mutu mwanga. Anali malingaliro okoma kudzamangitsa woyera ndi Yamikani koma maganizowo anabalalika tsiku ndinapezeka m’tchalichili, tsiku limene Yamikani anapereka umboni wake.

Tinakhala tcheru mkachisimo pamene bwezi langa Yamikani amapita kutsogolo. Sindinadabwe chifukwa anali atandiuzapo kuti tsiku lina adzapereka umboni wake m’tchalichimo. Koma ndikanadziwa kuti umboni wake ndiwotani, patsikuli sindikanapita kutchalichiko, ndikanamujedera pakhomo Satana.

“Abale anga wokondeka mwa Ambuye, ndili ndi nkhani ya moyo wanga imene ndigawane nanu, ndikhulupilira kuti itha kusinthanso miyoyo yanu” Anatsekulira motero umboni wakewo Yamikani. Anakamba zambiri za machimo amene amkachimwa mozemba. Aliyense m’kachisimo kuphatikizanso ine, anangogwira pakamwa, kudabwa. Sindimkayembekezera kumva zoterozo kuchokera kwa Yamikani. Anali machimo woopsa kwambiri. Zonsezitu silinali vuto loopsa kwambiri kwa ine, aliyense amachimwa. Koma chinandibalalitsa mutu kuti ndioneke ngati wopenga m’kachisi muja m’mawa wa tsikuli ndi chiganizo chimene chinatsendera umboni wa Yamikani.
“Ngati kulapa kwenikweni ndikupepesanso kwa wokondeka wanga Kolodiyo chifukwa nthawi yonseyi ndakhala ndikuyenda ndi amuna ena komanso ndinamupatsira nthenda ya masiku anoyi, Edzi. Mulungu andikhululukire.” Analitu Yamikani kubvumbulutsa chiganizo chimene chinasokoneza moyo wanga wonse. Kuti ndiwoneke ngati wolondola dzuwa m’kachisi muja ndi chifukwa cha chiganizochi. Ndinatuluka m’kachisimo nkhope nditagwetsa ngati namwali wokhatamizidwa ndi mvula ya mlango, nkhawa inali itandizinga ngati nsato m’thengo loyaka moto. Ndinazindikira koma mochedwa kwambiri kuti Yamikani anali Mfalisi wachiphamanso, njoka yaululu muudzu.
Ndimkapita kwathu kwa Chikang’a ndikulakatula kuti Demoni wotchedwa Yamikani wandidulira moyo

*Innocent Masina Nkhonyo………. (09268999)
Chancellor College
P.O. BOX 280
Zomba………< br>

DEMONI WOTCHEDWA YAMIKANI

Wolemba: Innocent Masina Nkhonyo*

Ndinadzambatuka pa mpando umene ndinakhala m’kachisimo ngati galu watsoka wopwanthamulidwa khofi ndi nyani wolusa ku uzimba. Ngakhale ndinabvumbuluka ngati katumbu wotsotsombetsedwa pa mbuto ndi ndodo yotchedwa banya, sindinaonetse zizindikiro za kumene ndinkafuna kulowera pa nthawiyo. Ndinamwaza maso anga pa nkhope za anthu m’kachisimo ndili chiyimile komatu ndikunjenjemera ngati chithumwa cha sing’anga wothana ndi athakati. Ndikanadziwa kuti maso a anthu onse amene anabwera kudzanyogodola satana m’kachisimo akhodzokera pa ine, sindikanayelekeza dala kuyimilira. Ndinaona akuluakulu ena akunong’onezana chapoteropo. Ndinadziwiratu kuti ankakambirana zoti andikwidzinge ndi zingwe poti zimene ndimkapanga nditangokumva umboni wa Yamikani zinali zifukwa zokwanira zokapezekera pa chipatala china cha anthu amzeru kwambiri ku Zomba. Ndindani akanakayikira kuti ziwala zinali zitayamba kuvina gule wa Mbotosha m’maso mwanga? Ngakhale anthu wodzapereka mathungwa achiyamiko kwa Chautawo anali ndi maganizo woti ndaduka mzengo, mwiniwakene ndimkadziwa kuti sichinali chiyambi cha misala. Zoona zake n’zakuti umboni wa Yamikani, mkazi yekhayo amene ndinamukhuthulira chikhulupiro changa chonse, unali utalasa mtima wanga. Zimene ndimkapangazo kunali kulephera kuvomereza zoona za umboniwo. Ngakhale ndimkadzichedwetsa kuvomera za umboni wosautsawo, ndinalibe mwayi wosankha. Zoona zake ndi zimene ananena msungwana wangayo Yamikani, nkhawena ya munthu, ndulu ya ng’ona, njoka muudzu, mfalisi wa chinyengo. Andikhululukire Mulungu wa Abraham chifukwa cha mayinawa koma mtima wanga woswekawu siwokozeka kukamba zabwino za Yamikani, mtsikana amene wandikumbira dzenje. Ndikamamaliza kusakatula masamba wofotokoza za ubwezi wanga ndi Yamikani mutsimikiza kuti mayina ndatchulawa ndiwomuyenera demoni ameneyu ndiponso muwonjezera ena pa amene alipo kalewa.

Ndinadziwana nayetu mtsikanayu, Yamikani pa nkhani za mayimbidwe. Anali m’kwaya imene imkatsitsimutsa anthu pa Tchalichi chathu cha Kapuso. Inenso ndinali m’kwaya yomweyo. Chikoka changa mwa mtsikanayo chitafika pa ndime yakuya sindinachedwa kutulutsa Chichewa chimene mamuna wina aliyense akanatulutsa kwa namwali wothwanima moyiwalitsa mikwingwilima ndi zitopotopo za m’dzikoli ngati Yamikani. Ngakhale anayamba wandigubitsako kwa timasiku ndithu anavomera kugwa m’chikondi nane.

Mbiri ya msungwana wangayu aliyense amkalalika kuyambira kumudzi kwawo ku Umodzi kudzamalizira patchalichipo. Kukakhala zochitika za kumpingo Yamikani amkapezeka kutsogolo kuyendetsa dongosolo lonse la miyambo ya uzimu. Atamandike chiumbiumbi Mulungu mwini chilengedwe chifukwa cha mphatso ya Yamikani, ilitu linali pemphero limene silimkatalikira makonde a mtima wanga.. sindimkachita manyazi kuwuza anzanga a m’mudzi wathu wa a Chikang’a kuti Yamikani adzakhala mayi wa ana anga.

Timkakondana mokolosa nsanje m’mitima ya mbeta komanso anyamata ambiri a mphala. Chikondi chathu chinali chomwera m’kapu imodzi chija cha sipa nane ndisipeko. Ndinamukhulupilira kwambiri Yamikani chifukwa tikakamba za asungwana angwiro m’dera lathu mfumukazi yawo inali duwa langali. Samkaopa kulangiza apuludzu wothothoka msidze, zimbayambaya ndi agong’oli wosowa mkhalidwe. Ambiritu anatembenuka chifukwa cha upangiri wa nyenyezi yanga Yamikani. Nanenso ngakhale anthu akwathu, Angoni, amalemekeza kachakumwa ka tsoo, ndinathetsa ubwezi wanga ndi mbiya ya Gamazula. Sindimkafuna kukhumudwitsa mnjelo wangayu, Yamikani.

Kuyezetsa magazi ndi bwezi lako ndi chinthu chimene masiku wowopsa ngati ano aliyense amalemekeza koma pakati pa ine ndi Yamikani panalibe chikayiko. Ngati ndinkhani yokayikiridwa, anali wokayikitsa ndi ine mwa awirife. Komatu naye Yamikani ananditsimikizira kuti samandikayikira choncho samaona chifukwa choti tikayezetsere magazi. Ngakhale zinali choncho chikhumbokhumbo choyezetsa magazi chibwezi chathu chisanafike potengerana kumayesero chimandipeza pafupipafupi. Sindimafuna kupereka matenda kwa bwezi langa choncho ndinakayezetsa magazi anga mwa mseri tisanayambe kugonana. Zotsatira zinali zosangalatsa, ndinalibe achikulilewo m’magazi anga. Izitu ndizimene ndimkayembekezera, ndimkakhulupilira kuti ngati ndili nako ndiye kuti ndinakatengera ku nsima chifukwa ngakhale poyamba ndimamwa kachakumwa, pa nkhani zotengerana m’gombezazi ndinali munthu wodzisunga. Nditadziwa zotsatira zanga tinayamba kupanga zonse zimene mwamuna ndi mkazi wokondana amachita kuphatikiza kufunditsana gombeza limodzi. Tinapitiriza kuyenda m’njira ya chikondi ndipo malingaliro wodzamangitsa woyera amkachita adodolido m’mutu mwanga. Anali malingaliro okoma kudzamangitsa woyera ndi Yamikani koma maganizowo anabalalika tsiku ndinapezeka m’tchalichili, tsiku limene Yamikani anapereka umboni wake.

Tinakhala tcheru mkachisimo pamene bwezi langa Yamikani amapita kutsogolo. Sindinadabwe chifukwa anali atandiuzapo kuti tsiku lina adzapereka umboni wake m’tchalichimo. Koma ndikanadziwa kuti umboni wake ndiwotani, patsikuli sindikanapita kutchalichiko, ndikanamujedera pakhomo Satana.

“Abale anga wokondeka mwa Ambuye, ndili ndi nkhani ya moyo wanga imene ndigawane nanu, ndikhulupilira kuti itha kusinthanso miyoyo yanu” Anatsekulira motero umboni wakewo Yamikani. Anakamba zambiri za machimo amene amkachimwa mozemba. Aliyense m’kachisimo kuphatikizanso ine, anangogwira pakamwa, kudabwa. Sindimkayembekezera kumva zoterozo kuchokera kwa Yamikani. Anali machimo woopsa kwambiri. Zonsezitu silinali vuto loopsa kwambiri kwa ine, aliyense amachimwa. Koma chinandibalalitsa mutu kuti ndioneke ngati wopenga m’kachisi muja m’mawa wa tsikuli ndi chiganizo chimene chinatsendera umboni wa Yamikani.
“Ngati kulapa kwenikweni ndikupepesanso kwa wokondeka wanga Kolodiyo chifukwa nthawi yonseyi ndakhala ndikuyenda ndi amuna ena komanso ndinamupatsira nthenda ya masiku anoyi, Edzi. Mulungu andikhululukire.” Analitu Yamikani kubvumbulutsa chiganizo chimene chinasokoneza moyo wanga wonse. Kuti ndiwoneke ngati wolondola dzuwa m’kachisi muja ndi chifukwa cha chiganizochi. Ndinatuluka m’kachisimo nkhope nditagwetsa ngati namwali wokhatamizidwa ndi mvula ya mlango, nkhawa inali itandizinga ngati nsato m’thengo loyaka moto. Ndinazindikira koma mochedwa kwambiri kuti Yamikani anali Mfalisi wachiphamanso, njoka yaululu muudzu.
Ndimkapita kwathu kwa Chikang’a ndikulakatula kuti Demoni wotchedwa Yamikani wandidulira moyo

*Innocent Masina Nkhonyo………. (09268999)
Chancellor College
P.O. BOX 280
Zomba………< br>SANANDIGWIRE SINDINALAKWE

Wolemba: Innocent Masina Nkhonyo*

“Aphedweee! Aphedweee! Aphedweeee! ” Tinayimba mwankokomo ngati mafunde olusa pa nyanja ya Malombe. Ndi mmene tinkaponyera mavume pa nyimbo za ntudzuzo palibe akanakhulupilira kuti nyimbozo tinkaziphunzilira pa chigulu pomwepo. Panthawiyi nkuti nthungo, zikwanje komanso madengu zili lakalaka. Ndinadabwa nditaona madenguwo koma nditaona njonda zina zikutapamo miyala, kudabwa konse kunabalalika. Ndikanadabwanso chiyani nditadziwonera ndekha ntchito ya zitetezo pa chifwilimbiticho?

Bwandiro, mnyamata amene amkasonkhezera chipwilikiticho kuti chifike pa ndime yakuya, amkatilondola chapatali. Samkasowekeranso kuti akhale kutsogolo pa nkhondo yothambitsa madolo achokoyo. Anayeneradi kusiyira ife ntchitoyo, gawo lalikulu anali atachita. Ngakhale ambiri mwa ife tinangotsatira chigulucho ndi miyala yathu m’manja, tinalibe zifukwa zenizeni zophwanyira nyumba za aphunzitsi athu. Anali ndi zifukwa zokwanira anali Bwandiro, mnyamata amene anatisonkhanitsa ndi kuyatsa moto waukali m’mitima yathu. Chifukwa cha lilime lake lodziwa kusoka mawu, tinapeza tizifukwa tingapo totsotsombetsera aphunsitsi athu.

Tinagwirizana zoyambira Nyumba ya mphuzitsi wamkulu kuyiphophola ndi alubwe amene tinasonkhanitsa. Balamanthu! kamwana kosapitilira zaka khumi kanatuluka m’nyumbamo. Kanali chibadwire. Ngakhale tinalakalaka titaseka palibe anayelekeza kuchita mano jee, kupichira ndudu yaphwete, iyitu siyinali nthawi ya nthabwala. Tinagwirizana zoyoyola Nyumba zonse pasukulupo ndipo chifukwa cha chiwelengero chathu sizinatitengele nthawi yayitali kukwanilitsa khumbo lathulo. titamaliza kulikita nyumbazo, tinalunjika ku mahositelo kukalisha akhakhakha amantha. Ndindani akanasekelera zoti ophunzira ena azibisala nthawi yomenyera ufulu ngati imeneyi? Ngati aliyense mwa ophunzirafe samkagwirizana ndi nkhanza zimene aphunzitsi athu amkatichira, n’chifukwa chiyani ena mwa ifenso anachiwona chamzeru kumabisala nthawi yowonetsa kusakondwa kwathu ndi mchitidwe wa aphunzitsiwo? . N’chifukwatu nafenso tinaona kuti anayeneradi kulandira mitechi isanu kapena kuwonjenzerapo afisi amantha amkabisalawo.

Tisanafike ku mahositelowo tinangoona galimoto zapolisi zisanu, munali aboma wovala zovala za mtundu wa therere. Zinali zachidziwikire kuti wina anayimba lamnya kuwadziwitsa a Polisiwo za chiwembucho kumene kunali kutiitanira nkhondo. Mosakhalitsa mfuti zinawombedwa, kuyimba nako kunazilara. Ena anayesa kuthawa koma nsapato za abomawo zinawabweza. Sindinadabwe nditawona ena akusisitira, mmene anaponyera miyendo a Polisiwo pa anyamatawo anangokhala ngati akupuntha anthu amsinkhu wawo. Ngakhale kunali kutangogwa mvula chakumene anatilamula kuti tikhale pasi. Tinakhaladi pamatope, ndiwolimba mtima uti amene akanawirungula pa maso pa nkhope zokwiyazo? “Za unkhutukumve mwachitazi mwawonetsa poyera kuti ndinu anthu wosayamika. Ndili ndi chinsoni kukuwuzani kuti ife sitingakwanitse kusunga mbalangondo zowononga sukulu yawo yomwe.” Tinakhala chete kumvetsela mwa chidwi kuti zitithera bwanji. Zoti aliyense wokhudzidwa amkanjenjemera pa malopo siyinali nkhani yochita kusoweka umboni. Munthu wa udindoyo anapuputa thukuta limene limatsika pa nkhope yake kumuchitira umboni kuti nyengoyo inalidi yosautsa. Atakhutira ndi tcheru lathulo anapitiriza. “Ndikudziwa kuti zikhala zowawa kwa inu kuvomera zimene ife tagwirizana, koma pepani kuti mukuyenerabe kuchita zimene muuzidwe poganizira kuti malo aliwonse amakhala ndi malamulo ake. Nonse apa mukudziwa kuti aliyense wophwanya lamulo amalangidwa moyenerana ndi chimene walakwilacho” Atafika pamenepa munthu waulamuliroyo ndinawona madzi akuyenderela pamene anakhala mnyamata wina kutsogola kwanga. Ndizoonadi kuti pamalopo panali matope chifukwa cha mvula imene inali itangokugwa chakumene komano sindikukhulupilira kuti panali madzi woti mpakana n’kuyendelera, ndi chifukwa chaketu sindinayenera kufunsa kuti madziwo amachokera kuti, ndinadziwilatu kuti mmodzi mwa ife analephera kuwongolera chilengedwe chake chifukwa cha ukali wa nyengowo. Ndithudi wina mwa ife anali atadzigwetsera mvula mkabudula. Panalibe amene anaseka kuti mzathuyo wakodzedwa, tonse tinamvetsa kuti nthawi ya chiweluzoyo inali nthawi yosokoneza ngakhale mmene amagwilira ntchito matupi athu.

Kenaka mkulu uja anapitiliza ndi mlango wakewo umenenso umafikano pa chiweluzo. “Tati titakhala pasi taganiza zokuchotsani sukulu nonse amene mukukhudzidwa ndi chipolowechi, apitiriza sukulu ndi anzanu anabisalawo. Ena mwa inu mukabweleranso chaka chamawa kudzabweleza m’makalasi mulimo koma n’zachidziwikire kuti enanu yatheratu potengera mmene mwakhala mukukhalira pasukulu pano. Muli ndi mphindi makumi awiri zokasonkhanitsira katundu wanu kumahositelo.” Anatsindika motero osati mphuzitsi wamkulu wa pasukulupo koma wamkulu wa zamaphunziro m’bomalo. Ndinadziwiliratu kuti awa anali mathero a ulendo wanga pasukulupo. Ndinalitu nditalandirapo chilango chokakhala kunyumba kwa mwezi wathunthu chifukwa cholanda ndalama ophunzira a kalasi yoyamba. Mbiri yanga siyinali yabwino, ndinadziwiratu kuti sadzandiyitananso kudzapitiriza maphunziro anga pasukulupo. Anzathu anabisala aja anapeleka nthumwi imodzi kuti iwayankhire mafunso.

Tonse tinadabwa titaona nthumwiyo. Sanali wina koma Bwandiro, Bwandiro wake yemwe uja anayambitsa chipoloweyu. Tinatulukira kuti mzathuyo anathawa ku zipolowe kuja ndikukabisala. Sizikanamvekanso zoti anayambitsa zitopotopozo anali mnyamatayo. “Ife titaona kuti amzathu akuphwanya sukulu tinapangana zoti tingobisala. Analipo ambiri ndipo sitikanalimbana nawo.” Anatero Bwandiro. Tithokoze kuti patsikulo kunacha bwino, ndithu kukanakhala kuti patsikulo kumatentha kwambiri, ena mwa ife tikanakomoka ndi mawuwo. Tinazindikira koma mochedwa kuti anatipeleka m’manja mwa adani anali munthu amene tinkasusa naye m’mbale imodzi. Ndinakanyamula tiakatundu tanga ulendo wa kwathu ku Mphunzi, ndimkapita ndikulingalira kuti aliyense amakhaladi wolakwa pokhapokha akagwidwa.


*Innocent Masina Nkhonyo
Chancellor College
P.O. Box 280
Zomba……09268999

ZA PAMOWA

Wolemba: Innocent Masina Nkhoyo*


Ndinakoka mpando wawutali pa malopo ndikudziponya mosangalala. Ndinali ndi chifukwa chokwanira chomwetulilira panthawiyo. Ndimkadziwa kuti wa masese wofululidwa mwa chingoni umenenso ndinawusowa kwa zaka zambiri upandidwa patsikulo.
“Amayi tathilani zisanu ziwiri zibwelere” Zoonadi kachetechete sawutsa nyama koma suyosuyo, anayimba wezuro Kwalirakape amene ife timkangoti Kwalira pomunyadira. Ukutu kunali kuyambitsa mwambo wopambanawo. Ndi Kwalirayutu amene amkakanyamula chakumwacho ife tili peche pa mpando mitu yathu ya panke titadendekera ngati agulo. Samawilingula kwalira. Akanatani munthu woti analibe ngakhala khobidi logulira ndudu ya Tom-tom. Kunyamula mapaketi achakumwacho inali mbali yokhayo imene Kwalira akanatenga pa gulu la matchona a kutawuni ngati ife.

Tinayamba kutsinkha molapitsa mowawo kwinaku nthabwala zikulikitimuka kukometsa mwambo wa chingoniwo. Nawo wodziwa kutakasa ziwuno anali chapoteropo kuthobotsa miyendo m’mwamba thukuta likuchucha ngati mtsinje wa Bua. Nawo anachiwona chanzeru kudzakometsa mwambowo.
“Koma m’mudzi mwathu muja amatipezelera ndithu” Anayifinya nkhani a Mbiyazapolama amene anakhala moyang’anana nane pa mwambo wopha chikokeyaniwo.
“Chadza ndiyani kuti dzina la mphunzitsi wa sukulu ya m’mudzi wa pantundapo lipezeke pa maina a anthu osauka a m’mudzi mwathu oti alandire nawo makoponi ogulira feteleza otsika mtengo? ” Anakhuthura maganinzo ake onse Mbiyazapolama kwinaku maso ali pa mtunda ngati wameza ng’oma ya nyau ija amati mbalule. Zinalidi zopweteka kuti anthu ena wophunzira amachita zachinyengozi kwa anthu wosauka popezerapo mwayi wa umphawi wawo. Ngakhale zinali choncho sindinathyolepo mnkhwani pa nkhaniyo. pajatu ndinali nditangofika kumene kumudziko kuchokera ku tawuni kumene ndinakatchona.

“Tabwerani apa a chimwene tilawe nawo timve kuti m’thupimu zikhala bwanji.” Uyu anali mayi wina amene anakhala pagulu la azimayi azake kuyitana njonda yina imene imangochita zungulizunguli pamolopo ndi thumba la mizu, zoperapera ndi timaphukusi ta mbwibwi zodziwa yekha. Ndimkaganizabe za kupezeka kwa amayiwo pa mowapo. Kenaka ndinakumbukira zimene anandiwuza Ndengundengu kuti pa chingoni amayi nawo amadzipeleka pa mwambo wolemekeza chakumwawo. Kenaka ndinawona amayi aja akulawa zimene njondayo imagulitsa mseko uli pakamwa.
“Ndilawe nawo amwene.” Uyu anali mnyamata amene anakhala pafupi ndi pamene pamachitikira malonda amphakapo.
“Choka! Uli ndi nkhali iwe kapena ufuna ukangotaya? ” Anakalipa mzimayi amene amawoneka wachikulirepo pagululo. Nditasinkhasinkha tanthaunzo la nkhali, ndinaumvera chinsoni mtundu wanga. Ndinazindikira chimene njonda yopanda manyaziyo imagulitsa. Kodi dzikoli likupita kuti? Ndinadzifunsa funso limene linandikanika kuyankha.
“Atuluke mapuyayo! ” Anamveka mawu. “nthumbidwa imeneyi yachokeranso kuti nanga? ” Anafunsa wina. “Umafuna uphunzilire pano eti? ” Sindinachitire mwini koma kuchewuka. Ndimkafuna kuwona chimene makosanawo amakuwiza. Amaseka ndoda ina imene imasanza chapoteropo. Chodabwitsa n’chakuti mmalo mosanza mowa mmene tonse timayembekezera, njondayo imasanza mitu ya micheni koma yosatafunidwa. Ndinadabwa koma nditakumbukira kuti pali amuna ena amene amalolera kumwa nyemba kachetechete wosatafuna kuti ana asadziwe, kudodoma kwanga konse kunabalarika. Ngakhale zinali zomvetsa chinsoni ndinalephera kuligwira phwete langa limene linandikakamiza kuchita zimene aliyense amachita pamalopo.

Titawonelera filimu ya wuleleyo tinakapitiliza mwambo wathu mokhulupirika. Pa nthawi yonse imene ndinakhala pa malopo ndimadabwa ndi m’kabwalo kena mmene amkapititsamo osati mapaketi a mowa koma ndowa za mowa. Ndinatchera khutu kuti ndimve zimene mabwana amayitanitsa ndowawo amakambirana.
“Ukawerenge buku la Yohane vesi sindikuwuza, amati Yesu anasandutsa madzi kukhala vinyo. Ndiye ife ndi ayani kuti tikanyoze chozwizwitsa choyamba cha mwana wa Mulungu? ” Ndinazindikira kuti amalankhulayo anali katswiri pa malembo woyera.
“Ifetu timangokumwa sitimaphunzitsa ana a ena uthakati” Anathilira ndemanga wina. Nditafufuza bwino za madolo amzeruwo, ndinazindikira kuti anali akuluakulu akumpingo kwathu kudzatenga nawo mbali mobisalira pa mwambo wolemekezekawo. Ndinakhumudwa zinali zachidziwikire kuti anthu a Mulunguwo amamwera chopeleka chathu chimene tinapeleka sabata imeneyo.
“Agalu, atchisi! Muli n’chiyani? Ndingathe kukudyetsani kuchokera pa wani mpakana sate. Ufiti eti? ! ” Uyu anali Kwalirakape kuyipidwa ndi khofi limene inamudzoza nalo njonda ina Kwalirakapeyo atayidzudzula kuti m’dengu la tomato la njondayo munapezeka kadzanja kamwana.
Ndinangomugwira pamkono Kwalirakapeyo pozindikira kuti izi zinali za pamowa. Ulendo wakunyumba unalinso womwewo.

*Innocent Masina Nkhonyo
P.O. Box 280
Zomba
09268999


Comments about Chikomekome Cha Mkuyu Ndi Nthano Zina by Innocent Masina Nkhonyo

There is no comment submitted by members..Read this poem in other languages

This poem has not been translated into any other language yet.

I would like to translate this poem »

word flags

What do you think this poem is about?Poem Submitted: Wednesday, December 17, 2008