Pa Khomo La Kachisi Poem by Judith Alekadala

Pa Khomo La Kachisi

Sizili bwino lero pano,
Inu anthu awa salankhula ndi opemphesa,
awopa kudetsedwa, iwo ndi opemphera,
mantha ananditha, posadziwa ndimvanji,
ndikadakhala ndi miyendo ndikadangoliyatsa.

Iwo changu chawo chikhala,
pakulowa mu kachisimu kukapembeza,
ndikuthamangilanso ku ma wanja awo,
amadzanditula pano achifundo,
kuti odutsa apa adzindiponyela limodzi, limodzi.

pamene mkuluyo anati penya kuno,
ndinachita changu kudzutsa mutu,
apo ndikulingalira kuti mwina ali nazo nazo,
koma anayamba ndi kuti;
Golide ndi siliva ndilibe!

Moyo wanga unayambanso kuthamanga,
pano ndiye molimbika zedi,
kodi akufuna chani akuluwa?
akufuna andichotse pano?
ndipita kuti tsono?

Anapitilira ndi kuti:
chomwe ndikupatse iwe ndi ichi,
mudzina la YESU WA KU NAZALETE
dzuka yenda!
Kodi akuluwa akunena Yesu yemwe anampachika uja?

Anandigwila dzanja munthu wopemphera wosaopa kudetsedwayu
mumtima ndinati ndiimilira choncho,
ngati chili chipongwe ndinazolowela,
koma ayi anthu inu ndinayamba kuyenda!
YESU anandiona ine pa khomo la kachisi
ngakhale pamene sindinali kumudziwa

COMMENTS OF THE POEM
READ THIS POEM IN OTHER LANGUAGES
Close
Error Success