Ndaima pa mwala
M'mbali mwa mtsinje kuyembekezera namwaliyo
Madzi achita liwiro, mphepo ikuwomba
Kampweya kayaziyazi kakudutsa
Ndiri chile kuyembekezera namwaliyo, inde wa pamtima panga
Suyo akubwerayo, ine tsembwe
Loto la Yosefe kundende
ine kumtima myaa!
Kafike kabuthu
Ine kuongola msana, iko kamvekere mwee!
Inu nkuti, langa langa
iko kakuti latonse
Chonena ndiribe
Mkanda wake mkhosi wauchotsa
Amvekere, ndiyang'ane
Ine kuti njoo! Loto lija latheka
Wauyamba ulendo
ine ndiri chete ngati nkhosa yokaphedwa
Kumulondora, iye amvekere, izi nzotani?
Ndapita, ndibwera usiku uno ngati maloto
Koma chonde msadzandiope, pakuti ndine amene
Ine nkuti, iwe dzipita
pakuti ndakupeza iwe wa pamtima panga
Bwera uzidzataya madzi ndakupeza.
Written by: Sandile *umhlaziyi Ozimele* Mngadi
Translated by: Sam Khulungira
Language: Chichewa
This poem has not been translated into any other language yet.
I would like to translate this poem