Mlomo Wanga Poem by Chikondi Daniel Dziko

Mlomo Wanga

Mlomo wanga
Sudzandiphurira ngozi Kodi?
Nchiani ukambazi?
Pali anthu akulu akulu Pano
Wakuuza ndani?

Abusa sanamvetu izi
Iwe waziba kuti?
Mbiyang'ambe ya mudzi
Ludzu lako naliwona
Kumtsinje wabibida
Iwe ndikabwerebwere

Iwe simlendo pamudzi Pano
Usandiuze wadza kamlomo wakuthwa
Sukadakhala chete kodi?
Palitu aneneri Pano
Nchiani ukambachi?

Oh Maine! Mlomo wanga
Wandiputilanji?
Oh Maine! Mlomo wanga
Ndilire bwanji?
Ndikudziwa mtima umawawa
Komabe ukanakhala chete

Ukambazi ulaula mtundu

COMMENTS OF THE POEM
READ THIS POEM IN OTHER LANGUAGES
Close
Error Success