Ndavomera Ndaima Pa Mwala M'Mbali Mwa Mtsinje Kuyembekezera Namwaliyo Madzi Achita Liwiro, Mphepo Ikuwomba Kampweya Kayaziyazi Kakudutsa Ndiri Chile Kuyembekezera Namwaliyo, Inde W Poem by Sandile mngadi.

Ndavomera Ndaima Pa Mwala M'Mbali Mwa Mtsinje Kuyembekezera Namwaliyo Madzi Achita Liwiro, Mphepo Ikuwomba Kampweya Kayaziyazi Kakudutsa Ndiri Chile Kuyembekezera Namwaliyo, Inde W

Rating: 5.0

Ndaima pa mwala
M'mbali mwa mtsinje kuyembekezera namwaliyo
Madzi achita liwiro, mphepo ikuwomba
Kampweya kayaziyazi kakudutsa
Ndiri chile kuyembekezera namwaliyo, inde wa pamtima panga

Suyo akubwerayo, ine tsembwe
Loto la Yosefe kundende
ine kumtima myaa!

Kafike kabuthu
Ine kuongola msana, iko kamvekere mwee!
Inu nkuti, langa langa
iko kakuti latonse
Chonena ndiribe

Mkanda wake mkhosi wauchotsa
Amvekere, ndiyang'ane
Ine kuti njoo! Loto lija latheka

Wauyamba ulendo
ine ndiri chete ngati nkhosa yokaphedwa
Kumulondora, iye amvekere, izi nzotani?
Ndapita, ndibwera usiku uno ngati maloto
Koma chonde msadzandiope, pakuti ndine amene
Ine nkuti, iwe dzipita
pakuti ndakupeza iwe wa pamtima panga
Bwera uzidzataya madzi ndakupeza.

Written by: Sandile *umhlaziyi Ozimele* Mngadi
Translated by: Sam Khulungira
Language: Chichewa

Monday, March 10, 2014
Topic(s) of this poem: love
POET'S NOTES ABOUT THE POEM
NDAVOMERA

Ndaima pa mwala
M'mbali mwa mtsinje kuyembekezera namwaliyo
Madzi achita liwiro, mphepo ikuwomba
Kampweya kayaziyazi kakudutsa
Ndiri chile kuyembekezera namwaliyo, inde wa pamtima panga

Suyo akubwerayo, ine tsembwe
Loto la Yosefe kundende
ine kumtima myaa!

Kafike kabuthu
Ine kuongola msana, iko kamvekere mwee!
Inu nkuti, langa langa
iko kakuti latonse
Chonena ndiribe

Mkanda wake mkhosi wauchotsa
Amvekere, ndiyang'ane
Ine kuti njoo! Loto lija latheka

Wauyamba ulendo
ine ndiri chete ngati nkhosa yokaphedwa
Kumulondora, iye amvekere, izi nzotani?
Ndapita, ndibwera usiku uno ngati maloto
Koma chonde msadzandiope, pakuti ndine amene
Ine nkuti, iwe dzipita
pakuti ndakupeza iwe wa pamtima panga
Bwera uzidzataya madzi ndakupeza.

Written by: Sandile *umhlaziyi Ozimele* Mngadi
Translated by: Sam Khulungira
Language: Chichewa
COMMENTS OF THE POEM
READ THIS POEM IN OTHER LANGUAGES
Close
Error Success