Innocent Masina Nkhonyo


Tcheru Achinyamata - Poem by Innocent Masina Nkhonyo

19…TCHERU ACHINYAMATA

Ndikamati tcheru achinyamata
Anu mapilikaniro muzitsekura
Usapitilire lako khonde uthengawu Nasuluma
Yako uchita sociolo ndi a tondewa
Mbamba ikundivundula ubongo
Ukachita milomo bwitibwiti
Lipistick atavinirapo gule wa chibwiza
Ukali wa unamwali ukukulamula zopusawo ukapitirila
M’theradi siudzasimba lozuna lija tsogolo
Akati kusintha mphongo
Ukutu ndiye kwanu kudya chemwali
M’kumati ukunjoya sidze utapenta zodziwa iwe ndi J-Lo
Ngati kachidzukulu ka Lusifa nuwoneke
Ati kutukwana chilengedwe haa zafika kwathu kuno

Kuvala nako n’zachidziwikire watayilira
Makamaka ukavala kako kaja ka mtosha
Ndinenatu kaja kovalira Lima
N’cholinga chofuna kuvumbulutsa milandu
Yovuta kuyipewa m’mbuyomu
Kwa za pa mphala ngwazi
Ukamayenda pakati panjonda
Zambiri mitu zikumabaizika
Modzipereka Makosi zikumathyola
Maso ali nyomi kuperekeza yako mbuyo yamwano
ikudzichitira yokha mabvume m’kabuluku kothinako uuhuu!
Kuti phedeguphedegu
Imvekere ma 25 ma 30, ma 25, ma 30
Komatu usosoka nawo tsitsi ma 25 amenewa.

Nawenso Motokosi bwera apa tsinibulu ndikoke khutulo
Ukachita kwevekweve ndi maganizo awupuludzuwo khodzokere
Mutu wa pamkewo dendekere
Ulendo wokabwira chamba zidzete
Usamayese ndi udolo m’phwanga
Potitu ambiri akadya oterewu utsi
Chibwana chadzawoneni akuponda mu m’tsuko
Chimachita dzeka m’mitu yopusayo
Amakaikodola ya moto juu mbonawona
Pokhutitsana chikondi ndi Aulendowu n’watonse
Kuyiwala kuti kuli yothobotsa kufwendekera nthenda
Komano balamanthu ikadzavumbuluka Edzi
N’pamene adzadziwe kuti dzikoli n’chitedze
Mbamba achibwana limasisimitsa
Akagundika kuwukanyanga mlakatuli uphungu
Musamabwatikane kuti wapapira uja wa ukali mtonjane
Konsekutu n’kukuchengeterani lanu tsogolo
Kuti chija cha m’dzamtengezeni chuma
Ndithudi chisadzakuphonyeni
Koma mukanyozera madolo inu
Ya matenda mikwingwirima ndiyo m’maso idzakutsulukuteni
Itapanilira kukuvinitsani chimtali Edzi
Matewera atayamba kukukulungani
Haaa Wodalirikawo mabuleki atakhwefuka
Kukusungirani wotayika kale ulemu
A unkhutukumve manyozo akuchita chipako pa zoumbazo nkhope
Tsono ndikamati tcheru, inu muzikhala tcheru.


Comments about Tcheru Achinyamata by Innocent Masina Nkhonyo

There is no comment submitted by members..Read this poem in other languages

This poem has not been translated into any other language yet.

I would like to translate this poem »

word flags

What do you think this poem is about?Poem Submitted: Wednesday, January 21, 2009[Report Error]